Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 21:12 - Buku Lopatulika

12 Yesu ananena nao, Idzani mufisule. Koma palibe mmodzi wa ophunzira anatha kumfunsa Iye, Ndinu yani? Podziwa kuti ndiye Ambuye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Yesu ananena nao, Idzani mufisule. Koma palibe mmodzi wa ophunzira anatha kumfunsa Iye, Ndinu yani? Podziwa kuti ndiye Ambuye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Yesu adaŵauza kuti, “Bwerani, mufisule.” Koma mwa ophunzirawo panalibe ndi mmodzi yemwe amene adaalimba mtima kumufunsa kuti, “Ndinu yani?” Pakuti adaazindikira kuti ndi Ambuye.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Yesu anawawuza kuti, “Bwerani mudzalandire chakudya chammawa.” Palibe mmodzi wa ophunzira anayesa kumufunsa Iye, “Kodi ndinu ndani?” Iwo anadziwa kuti anali Ambuye.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 21:12
9 Mawu Ofanana  

Ndipo sanalimbike mtima munthu aliyense kumfunsa kanthu kuyambira tsiku lomwelo.


Koma iwo sanazindikire mauwo, naopa kumfunsa.


Koma iwo sanadziwitse mau awa, ndipo anabisidwa kwa iwo, kuti asawadziwe; ndipo anaopa kumfunsa za mau awa.


Yesu anazindikira kuti analikufuna kumfunsa Iye, ndipo anati kwa iwo, Kodi mulikufunsana wina ndi mnzake za ichi, kuti ndinati, Kanthawi ndipo simundiona Ine, ndiponso kanthawi nimudzandiona Ine?


Chifukwa chake Simoni Petro anakwera m'ngalawa nakokera khoka kumtunda lodzala ndi nsomba zazikulu, zana limodzi, ndi makumi asanu ndi zitatu; ndipo zingakhale zinachuluka kotere, kokha silinang'ambika.


Ndipo pamene atafisula Yesu ananena kwa Simoni Petro, Simoni mwana wa Yona, kodi undikonda Ine koposa awa? Ananena ndi Iye, Inde, Ambuye; mudziwa kuti ndikukondani Inu. Ananena naye, Dyetsa anaankhosa anga.


Ndipo pamenepo anadza ophunzira ake; nazizwa kuti analinkulankhula ndi mkazi; koma panalibe wina anati, Mufuna chiyani? Kapena, mulankhula naye chiyani?


si kwa anthu onse ai, koma kwa mboni zosankhidwiratu ndi Mulungu, ndiwo ife amene tinadya ndi kumwa naye pamodzi, atauka iye kwa akufa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa