Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 2:23 - Buku Lopatulika

23 Koma pamene anali mu Yerusalemu pa Paska pachikondwerero, ambiri anakhulupirira dzina lake, pakuona zizindikiro zake zimene anachitazi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 Koma pamene anali m'Yerusalemu pa Paska pachikondwerero, ambiri anakhulupirira dzina lake, pakuona zizindikiro zake zimene anachitazi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 Pamene Yesu anali m'Yerusalemu pa chikondwerero cha Paska, anthu ambiri adayamba kuika chikhulupiriro chao pa Iye, poona zozizwitsa zimene ankachita.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 Tsopano Iye ali mu Yerusalemu pa phwando la Paska, anthu ambiri anaona zizindikiro zodabwitsa zimene amachita ndipo anakhulupirira dzina lake.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 2:23
18 Mawu Ofanana  

Ndipo za pathanthwe ndiwo amene, pakumva, alandira mau ndi kukondwera; koma alibe mizu; akhulupirira kanthawi, ndipo pa nthawi ya mayesedwe angopatuka.


Chifukwa chake ambiri a mwa Ayuda amene anadza kwa Maria, m'mene anaona chimene anachita, anakhulupirira Iye.


Chiyambi ichi cha zizindikiro zake Yesu anachita mu Kana wa mu Galileya naonetsera ulemerero wake; ndipo ophunzira ake anakhulupirira Iye.


Ndipo Paska wa Ayuda unayandikira, ndipo Yesu anakwera kunka ku Yerusalemu.


Iyeyu anadza kwa Yesu usiku, nati kwa Iye, Rabi, tidziwa kuti Inu ndinu mphunzitsi wochokera kwa Mulungu; pakuti palibe munthu akhoza kuchita zizindikiro zimene Inu muchita, ngati Mulungu sakhala naye.


Chifukwa chake pamene anadza ku Galileya, Agalileya anamlandira Iye, atakaona zonse zimene anazichita mu Yerusalemu pachikondwerero; pakuti iwonso ananka kuchikondwerero.


Koma Ine ndili nao umboni woposa wa Yohane; pakuti ntchito zimene Atate anandipatsa ndizitsirize, ntchito zomwezo ndizichita zindichitira umboni, kuti Atate anandituma Ine.


Chifukwa chake, anthu, poona chizindikiro chimene anachita, ananena, kuti, Ameneyo ndiye mneneri ndithu wakudzayo m'dziko lapansi.


Ndipo khamu lalikulu la anthu linamtsata Iye, chifukwa anaona zizindikiro zimene anachita pa odwala.


Koma ambiri a m'khamu la anthu anakhulupirira Iye; ndipo ananena, Pamene Khristu akadza kodi adzachita zizindikiro zambiri zoposa zimene adazichita ameneyo?


Pakuti mwa Khristu Yesu kapena mdulidwe kapena kusadulidwa kulibe mphamvu; komatu chikhulupiriro, chakuchititsa mwa chikondi.


Ndipo lamulo lake ndi ili, kuti tikhulupirire dzina la Mwana wake Yesu Khristu, ndi kukondana wina ndi mnzake monga anatilamulira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa