Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 19:9 - Buku Lopatulika

9 Ndipo analowanso ku Pretorio, nanena kwa Yesu, Muchoka kuti? Koma Yesu sanamyankhe kanthu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo analowanso ku Pretorio, nanena kwa Yesu, Muchoka kuti? Koma Yesu sanamyankha kanthu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Tsono adaloŵanso m'nyumba ya bwanamkubwa ija nafunsa Yesu kuti, “Kodi iwe, kwanu nkuti?” Koma Yesu sadayankhe kanthu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 ndipo anabwereranso mʼnyumba yaufumu. Iye anafunsa Yesu kuti, “Kodi umachokera kuti?” Koma Yesu sanayankhe.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 19:9
18 Mawu Ofanana  

Iye anatsenderezedwa koma anadzichepetsa yekha osatsegula pakamwa pake; ngati nkhosa yotsogoleredwa kukaphedwa, ndi ngati mwanawankhosa amene ali duu pamaso pa omsenga, motero sanatsegule pakamwa pake.


Koma Yesu anangokhala chete. Ndipo mkulu wa ansembe ananena kwa Iye, Ndikulumbiritsa Iwe pa Mulungu wamoyo, kuti utiuze ife ngati Iwe ndiwe Khristu, Mwana wa Mulungu.


Pomwepo asilikali a kazembe anamuka naye Yesu kubwalo la milandu, nasonkhanitsa kwa Iye khamu lao lonse.


Ndipo anamfunsa Iye mau ambiri; koma Iye sanamyankhe kanthu.


Pamenepo anamtenga Yesu kuchokera kwa Kayafa kupita ku Pretorio; koma munali mamawa; ndipo iwo sanalowe ku Pretorio, kuti angadetsedwe, koma kuti akadye Paska.


Chifukwa chake Pilato analowanso mu Pretorio, naitana Yesu, nati kwa Iye, Iwe ndiwe mfumu ya Ayuda kodi?


Yesu anayankha, Kodi munena ichi mwa inu nokha, kapena ena anakuuzani za Ine?


Pamenepo Pilato anati kwa Iye, Nanga kodi ndiwe Mfumu? Yesu anayankha, Munena kuti ndine Mfumu. Ndinabadwira ichi Ine, ndipo ndinadzera ichi kudza kudziko lapansi, kuti ndikachite umboni ndi choonadi. Yense wakukhala mwa choonadi amva mau anga.


Chifukwa chake Pilato ananena kwa Iye, Simulankhula ndi ine kodi? Simudziwa kodi kuti ulamuliro ndili nao wakukumasulani, ndipo ndili nao ulamuliro wakukupachikani?


Ndipo pamene Pilato anamva mau awa, anaopa koposa.


Anayankha Yesu nati kwa iwo, Ndingakhale ndichita umboni wa Ine ndekha umboni wanga uli woona; chifukwa ndidziwa kumene ndinachokera ndi kumene ndimukako; koma inu simudziwa kumene ndichokera, ndi kumene ndimukako.


osaopa adani m'kanthu konse, chimene chili kwa iwowa chisonyezo cha chionongeko, koma kwa inu cha chipulumutso, ndicho cha kwa Mulungu;


Pamenepo anadza mkaziyo, nanena ndi mwamuna wake ndi kuti, Wandidzera munthu wa Mulungu; maonekedwe ake ndiwo ngati maonekedwe a mthenga wa Mulungu oopsa ndithu; ndipo sindinamfunse uko achokera kapena sanandiuzenso dzina lake;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa