Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 19:41 - Buku Lopatulika

41 Koma kunali munda kumalo kumene anapachikidwako, ndi m'mundamo munali manda atsopano m'mene sanaikidwemo munthu aliyense nthawi zonse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

41 Koma kunali munda kumalo kumene anapachikidwako, ndi m'mundamo munali manda atsopano m'mene sanaikidwamo munthu aliyense nthawi zonse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

41 Kumene Yesu adaapachikidwako kunali munda. Ndipo m'mundamo munali manda atsopano, amene anali asanaikemo munthu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

41 Pamalo pamene anapachikidwa Yesu panali munda ndipo mʼmundamo munali manda atsopano mʼmene munali simunayikidwemo aliyense.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 19:41
7 Mawu Ofanana  

Ndipo anyamata ake anamtengera wakufa m'galeta, nabwera naye ku Yerusalemu kuchokera ku Megido, namuika m'manda akeake. Ndipo anthu a m'dziko anatenga Yehowahazi mwana wa Yosiya, namdzoza, namlonga ufumu m'malo mwa atate wake.


Uchitanji iwe kuno, ndimo ndani ali nawe kuno, kuti iwe wagoba manda kuno, ndi kudzigobera manda pamwamba, ndi kudzisemera mogonamo m'thanthwe.


nauika m'manda ake atsopano, osemedwa m'mwala, nakunkhunizira mwala waukulu pakhomo pa manda, nachokapo.


Ndipo anautsitsa, naukulunga m'nsalu yabafuta, nauika m'manda osemedwa m'mwala, m'menemo sanaike munthu ndi kale lonse.


Pomwepo ndipo anaika Yesu, chifukwa cha tsiku lokonzera la Ayuda, pakuti mandawo anali pafupi.


Yesu ananena naye, Mkazi, uliranji? Ufuna yani? Iyeyu poyesa kuti ndiye wakumunda, ananena ndi Iye, Mbuye ngati mwamnyamula Iye, ndiuzeni kumene mwamuika Iye, ndipo ndidzamchotsa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa