Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yohane 19:42 - Buku Lopatulika

42 Pomwepo ndipo anaika Yesu, chifukwa cha tsiku lokonzera la Ayuda, pakuti mandawo anali pafupi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

42 Pomwepo ndipo anaika Yesu, chifukwa cha tsiku lokonzera la Ayuda, pakuti mandawo anali pafupi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

42 Tsono popeza kuti linali tsiku la Ayuda lokonzekera chikondwerero cha Paska, ndipo mandawo anali pafupi, adaika Yesu m'menemo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

42 Chifukwa linali Tsiku la Ayuda Lokonzekera ndi kuti mandawo anali pafupipo, iwo anayika Yesu mʼmenemo.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 19:42
10 Mawu Ofanana  

Mphamvu yanga yauma ngati phale; ndi lilime langa likangamira kunsaya zanga; ndipo mwandifikitsa kufumbi la imfa.


Ndipo anaika manda ake pamodzi ndi oipa, ndi pamodzi ndi olemera mu imfa yake, ngakhale Iye sanachite chiwawa, ndipo m'kamwa mwake munalibe chinyengo.


pakuti monga Yona anali m'mimba mwa chinsomba masiku atatu ndi usiku wake, chomwecho Mwana wa Munthu adzakhala mumtima mwa dziko lapansi masiku atatu ndi usiku wake.


Koma linali tsiku lokonza Paska; panali monga ora lachisanu ndi chimodzi. Ndipo ananena kwa Ayuda, Taonani, mfumu yanu!


Ndipo lembo ilo analiwerenga ambiri a Ayuda; chifukwa malo amene Yesu anapachikidwapo anali pafupi pa mzindawo; ndipo linalembedwa mu Chihebri, ndi mu Chilatini, ndi mu Chigriki.


Pomwepo Ayuda, popeza panali tsiku lokonzera, kuti mitembo ingatsale pamtanda tsiku la Sabata, pakuti tsiku lomwelo la Sabata linali lalikulu, anapempha Pilato kuti miyendo yao ithyoledwe, ndipo achotsedwe.


Koma kunali munda kumalo kumene anapachikidwako, ndi m'mundamo munali manda atsopano m'mene sanaikidwemo munthu aliyense nthawi zonse.


Ndipo atatsiriza zonse zolembedwa za Iye, anamtsitsa kumtengo, namuika m'manda.


ndi kuti anaikidwa; ndi kuti anaukitsidwa tsiku lachitatu, monga mwa malembo;


popeza munaikidwa m'manda pamodzi ndi Iye muubatizo, momwemonso munaukitsidwa pamodzi ndi Iye m'chikhulupiriro cha machitidwe a Mulungu, amene anamuukitsa Iye kwa akufa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa