Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 18:11 - Buku Lopatulika

11 Pamenepo Yesu anati kwa Petro, Longa lupanga m'chimake chake; chikho chimene Atate wandipatsa Ine sindimwere ichi kodi?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Pamenepo Yesu anati kwa Petro, Longa lupanga m'chimake chake; chikho chimene Atate wandipatsa Ine sindimwere ichi kodi?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Apo Yesu adauza Petro kuti, “Bwezera lupanga lako m'chimake. Kodi ukuti ndisamwe chikho cha masautso chimene Atate andipatsa?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Yesu analamula Petro kuti, “Bwezera lupanga mʼchimake! Kodi Ine ndisamwere chikho chimene Atate andipatsa?”

Onani mutuwo Koperani




Yohane 18:11
22 Mawu Ofanana  

Mfumu niti, Ndili ndi chiyani ndi inu, ana a Zeruya? Pakuti atukwana, ndi pakuti Yehova ananena naye, Utukwane Davide; ndani tsono adzanena, Watero chifukwa ninji?


Pakuti m'dzanja la Yehova muli chikho; ndi vinyo wake achita thovu; chidzala ndi zosakanizira, ndipo atsanulako. Indedi, oipa onse a padziko lapansi adzamwa nadzagugudiza nsenga zake.


Wayenda m'njira ya mkulu wako, chifukwa chake ndidzapereka chikho chake m'dzanja lako.


Koma Yesu anayankha nati, Inu simudziwa chimene mupempha. Kodi mukhoza kumwera chikho nditi ndidzamwere Ine? Iwo ananena kwa Iye, Ife tikhoza.


Ndipo anamuka patsogolo pang'ono, nagwa nkhope yake pansi, napemphera, nati, Atate ngati nkutheka, chikho ichi chindipitirire Ine; koma si monga ndifuna Ine, koma Inu.


Anamukanso kachiwiri, napemphera, nati, Atate wanga, ngati ichi sichingandipitirire, koma ndimwere ichi, kufuna kwanu kuchitidwe.


Pakuti izi zonse mitundu ya anthu a padziko lapansi amazifunafuna; koma Atate wanu adziwa kuti musowa zimenezi.


nati, Atate, mukafuna Inu, chotsani chikho ichi pa Ine; koma si kufuna kwanga ai, komatu kwanu kuchitike.


Ngati musunga malamulo anga mudzakhala m'chikondi changa; monga Ine ndasunga malamulo a Atate wanga, ndipo ndikhala m'chikondi chake.


Atate, amene mwandipatsa Ine, ndifuna kuti, kumene ndili Ine, iwonso akhale pamodzi ndi Ine; kuti ayang'anire ulemerero wanga, umene mwandipatsa Ine; pakuti munandikonda Ine lisanakhazikike dziko lapansi.


Yesu anayankha, Ufumu wanga suli wa dziko lino lapansi; ufumu wanga ukadakhala wa dziko lino lapansi, anyamata anga akadalimbika nkhondo, kuti ndisaperekedwe kwa Ayuda; koma tsopano ufumu wanga suli wochokera konkuno.


Yesu ananena naye, Usandikhudze, pakuti sinditha kukwera kwa Atate; koma pita kwa abale anga, ukati kwa iwo, Ndikwera kunka kwa Atate wanga, ndi Mulungu wanu.


(pakuti zida za nkhondo yathu sizili za thupi, koma zamphamvu mwa Mulungu zakupasula malinga);


m'mau a choonadi, mu mphamvu ya Mulungu; mwa zida za chilungamo kulamanja ndi kulamanzere,


Yesu, ameneyo, chifukwa cha chimwemwe choikidwacho pamaso pake, anapirira mtanda, nanyoza manyazi, nakhala padzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa