Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 17:4 - Buku Lopatulika

4 Ine ndalemekeza Inu padziko lapansi, m'mene ndinatsiriza ntchito imene munandipatsa ndichite.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ine ndalemekeza Inu pa dziko lapansi, m'mene ndinatsiriza ntchito imene munandipatsa ndichite.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Ndakulemekezani pansi pano pakutsiriza ntchito imene mudandipatsa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Ine ndabweretsa ulemerero wanu pa dziko pamene ndamaliza ntchito imene munandipatsa kuti ndi igwire.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 17:4
13 Mawu Ofanana  

Pakuti ndinena ndi inu, chimene chidalembedwa chiyenera kukwanitsidwa mwa Ine, Ndipo anawerengedwa ndi anthu opanda lamulo; pakuti izi za kwa Ine zili nacho chimaliziro.


Atate, lemekezani dzina lanu. Pomwepo adadza mau ochokera Kumwamba, Ndalilemekeza, ndipo ndidzalilemekezanso.


Ndipo chimene chilichonse mukafunse m'dzina langa, ndidzachichita, kuti Atate akalemekezedwe mwa Mwana.


koma kuti dziko lapansi lizindikire kuti ndikonda Atate, ndi kuti ndichita monga momwe Atate wandilamula. Nyamukani, tizimuka kuchokera kuno.


Ngati musunga malamulo anga mudzakhala m'chikondi changa; monga Ine ndasunga malamulo a Atate wanga, ndipo ndikhala m'chikondi chake.


Chitapita ichi Yesu, podziwa kuti zonse zidatha pomwepo kuti lembo likwaniridwe, ananena, Ndimva ludzu.


Pamene Yesu tsono adalandira vinyo wosasayo anati, Kwatha; ndipo anawerama mutu, napereka mzimu.


Yesu ananena nao, Chakudya changa ndicho kuti ndichite chifuniro cha Iye amene anandituma Ine, ndi kutsiriza ntchito yake.


Koma Ine ndili nao umboni woposa wa Yohane; pakuti ntchito zimene Atate anandipatsa ndizitsirize, ntchito zomwezo ndizichita zindichitira umboni, kuti Atate anandituma Ine.


Yesu anayankha, Sanachimwe ameneyo, kapena atate wake ndi amake; koma kuti ntchito za Mulungu zikaonetsedwe mwa iye.


Komatu sindiuyesa kanthu moyo wanga, kuti uli wa mtengo wake kwa ine ndekha; kotero kuti ndikatsirize njira yanga, ndi utumiki ndinaulandira kwa Ambuye Yesu, kuchitira umboni Uthenga Wabwino wa chisomo cha Mulungu.


Ndalimbana nako kulimbana kwabwino, ndatsiriza njirayo, ndasunga chikhulupiriro:


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa