Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 16:32 - Buku Lopatulika

32 Onani ikudza nthawi, ndipo yafika, imene mudzabalalitsidwa, yense ku zake za yekha, ndipo mudzandisiya Ine pa ndekha. Ndipo sindikhala pa ndekha, chifukwa Atate ali pamodzi ndi Ine,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

32 Onani ikudza nthawi, ndipo yafika, imene mudzabalalitsidwa, yense ku zake za yekha, ndipo mudzandisiya Ine pa ndekha. Ndipo sindikhala pa ndekha, chifukwa Atate ali pamodzi ndi Ine,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

32 Nthaŵi ilikudza, ndipo yafika kale, pamene mudzabalalikana aliyense kunka kwao, Ine kundisiya ndekha. Komabe sindili ndekha, pakuti Atate ali nane.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

32 Koma nthawi ikubwera ndipo yafika, pamene inu mudzabalalitsidwa, aliyense ku nyumba yake. Inu mudzandisiya ndekhandekha. Koma Ine sindili ndekha, pakuti Atate anga ali nane.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 16:32
22 Mawu Ofanana  

Galamuka, lupanga, pa mbusa wanga, ndi pa munthu mnzanga wa pamtima, ati Yehova wa makamu; kantha mbusa, ndi nkhosa zidzabalalika; koma ndidzabwezera dzanja langa pa zazing'onozo.


Pamenepo Yesu ananena kwa iwo, Inu nonse mudzakhumudwa chifukwa cha Ine usiku uno; pakuti kwalembedwa, Ndidzakantha mbusa, ndipo zidzabalalika nkhosa za gulu.


Koma izi zonse zinachitidwa, kuti zolembedwa za aneneri zikwaniridwe. Pomwepo ophunzira onse anamsiya Iye, nathawa.


Ndipo Yesu ananena nao, Mudzakhumudwa nonsenu; pakuti kwalembedwa, Ndidzakantha mbusa, ndi nkhosa zidzamwazika.


Ndipo iwo onse anamsiya Iye, nathawa.


Koma Yesu anayankha iwo, nati, Yafika nthawi, kuti Mwana wa Munthu alemekezedwe.


Adzakutulutsani m'masunagoge, koma ikudza nthawi imene yense wakupha inu adzayesa kuti atumikira Mulungu.


Zinthu izi ndalankhula ndi inu m'mafanizo; ikudza nthawi imene sindidzalankhula ndi inu m'mafanizo, koma ndidzakulalikirani inu m'mafanizo, koma ndidzakulalikirani inu momveka za Atate.


Yesu anayankha iwo, Kodi mukhulupirira tsopano?


Pamene ananena kwa wophunzirayo, Taona, amai wako. Ndipo kuyambira ora lomweli wophunzirayo ananka naye kwao.


Chifukwa chake ophunzirawo anachokanso, kunka kwao.


Yesu ananena naye, Tamvera Ine, mkazi iwe, kuti ikudza nthawi, imene simudzalambira Atate kapena m'phiri ili, kapena mu Yerusalemu.


Koma ikudza nthawi, ndipo tsopano ilipo, imene olambira oona adzalambira Atate mumzimu ndi m'choonadi; pakuti Atate afuna otere akhale olambira ake.


Indetu, indetu, ndinena kwa inu, kuti ikudza nthawi, ndipo ilipo tsopano, imene akufa adzamva mau a Mulungu; ndipo iwo akumva adzakhala ndi moyo.


Musazizwe ndi ichi, kuti ikudza nthawi, imene onse ali m'manda adzamva mau ake,


Ndipo ngati ndiweruza Ine, chiweruziro changa chili choona; pakuti sindili pa ndekha, koma Ine ndi Atate amene anandituma Ine.


Ndipo wondituma Ine ali ndi Ine; sanandisiye Iye pa ndekha; chifukwa ndichita Ine zimene zimkondweretsa Iye nthawi zonse.


ndi kulawirana; ndipo tinalowa m'ngalawa, koma iwo anabwera kwao.


Ndipo Saulo analikuvomerezana nao pa imfa yake. Ndipo tsikulo kunayamba kuzunza kwakukulu pa Mpingo unali mu Yerusalemu; ndipo anabalalitsidwa onse m'maiko a Yudeya ndi Samariya, koma osati atumwi ai.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa