Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 15:6 - Buku Lopatulika

6 Ngati wina sakhala mwa Ine, watayika kunja monga nthambi, nafota; ndipo azisonkhanitsa nazitaya kumoto, nazitentha.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ngati wina sakhala mwa Ine, watayika kunja monga nthambi, nafota; ndipo azisonkhanitsa nazitaya kumoto, nazitentha.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Ngati munthu sakhala mwa Ine, amamtaya kunja monga nthambi yodulidwa, ndipo amauma. Nthambi zotere amazitola, naziponya pa moto ndipo zimapsa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Ngati wina aliyense sakhala mwa Ine, iyeyo ali ngati nthambi imene yatayidwa ndi kufota. Nthambi zotero zimatoledwa, kuponyedwa pa moto ndi kupsa.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 15:6
20 Mawu Ofanana  

koma wakukhudza iyo adzikonzeratu chitsulo ndi luti la mkondo; ndipo idzatenthedwa konse ndi moto m'malo mwao.


Sadzachoka mumdima; lawi la moto lidzaumitsa nthambi zake; ndipo adzachoka ndi mpumo wa m'kamwa mwake.


ndi tsinde limene dzanja lanu lamanja linaoka, ndi mphanda munadzilimbikitsira.


Koma iwe watayidwa kunja kwa manda ako, ngati nthambi yonyansa, ngati chovala cha ophedwa, opyozedwa ndi lupanga, otsikira kumiyala ya dzenje, monga ngati mtembo wopondedwa ndi phazi.


Pakuti mzinda wotchingidwa uli pa wokha, mokhalamo mwa bwinja, ndi mosiyidwa ngati chipululu; mwanawang'ombe adzadya kumeneko, nadzagonako pansi, nadzamaliza nthambi zake.


Uziti, Atero Ambuye Yehova, Udzakondwa kodi? Sadzausula ndi kudula zipatso zake, kuti uume, kuti masamba ake onse ophuka aume, ngakhale palibe mphamvu yaikulu, kapena anthu ambiri akuuzula?


Mwana wa Munthu adzatuma angelo ake, ndipo iwo adzasonkhanitsa pamodzi, ndi kuchotsa mu Ufumu wake zokhumudwitsa zonse, ndi anthu akuchita kusaweruzika,


Ndipo iye anataya pansi ndalamazo pa Kachisi, nachokapo, nadzipachika yekha pakhosi.


Ndiponso tsopano lino nkhwangwa yaikidwa pa mizu ya mitengo: chifukwa chake mtengo uliwonse wosabala zipatso zabwino udulidwa nuponyedwa pamoto.


Mtengo uliwonse wosapatsa chipatso chokoma, audula, nautaya kumoto.


Nthambi iliyonse ya mwa Ine yosabala chipatso, aichotsa; ndi iliyonse yakubala chipatso, aisadza, kuti ikabale chipatso chochuluka.


koma kulindira kwina koopsa kwa chiweruziro, ndi kutentha kwake kwa moto wakuononga otsutsana nao.


Pakuti ngati, adatha kuthawa zodetsa za dziko lapansi mwa chizindikiritso cha Ambuye ndi Mpulumutsi Yesu Khristu, akondwanso nazo, nagonjetsedwa, zotsiriza zao zidzaipa koposa zoyambazo.


Anatuluka mwa ife, komatu sanali a ife; pakuti akadakhala a ife akadakhalabe ndi ife, koma kudatero kuti aonekere kuti sali onse a ife.


Ndipo ngati munthu sanapezedwe wolembedwa m'buku la moyo, anaponyedwa m'nyanja yamoto.


Koma amantha, ndi osakhulupirira, ndi onyansa, ndi ambanda, ndi achigololo, ndi olambira mafano, ndi onse a mabodza, cholandira chao chidzakhala m'nyanja yotentha ndi moto ndi sulufure; ndiyo imfa yachiwiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa