Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 15:1 - Buku Lopatulika

1 Ine ndine mpesa weniweni, ndipo Atate wanga ndiye wam'munda.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ine ndine mpesa weniweni, ndipo Atate wanga ndiye wam'munda.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 “Ine ndine mpesa weniweni, ndipo Atate anga ndi mlimi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 “Ine ndine mpesa weniweni, ndipo Atate anga ndiye mwini munda.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 15:1
28 Mawu Ofanana  

Tilawire kunka kuminda yamipesa; tiyang'ane ngati mpesa waphuka, kunje ndi kuonetsa zipatso, makangaza ndi kutuwa maluwa ake; pompo ndidzakupatsa chikondi changa.


Tsiku limenelo mphukira ya Yehova idzakhala yokongola ndi ya ulemerero, chipatso cha nthaka chidzakhala chokometsetsa ndi chokongola, kwa iwo amene adzapulumuka a Israele.


Anthu ako adzakhalanso onse olungama; dzikolo lidzakhala cholowa chao kunthawi zonse, nthambi yooka Ine, ntchito ya manja anga, kuti Ine ndikuzidwe.


ndikakonzere iwo amene alira maliro mu Ziyoni, ndi kuwapatsa chovala kokometsa m'malo mwa phulusa, mafuta akukondwa m'malo mwa maliro, chovala cha matamando m'malo mwa mzimu wopsinjika; kuti iwo atchedwe mitengo ya chilungamo yakuioka Yehova, kuti Iye alemekezedwe.


Abusa ambiri aononga munda wanga wampesa, apondereza gawo langa, pondikondweretsa apayesa chipululu chopanda kanthu.


Ndipo Ine ndinakuoka mpesa wangwiro, mbeu yoona; kodi bwanji wandisandukira Ine mbeu yopanda pake, ya mpesa wachilendo?


Mai wako ananga mpesa wookedwa kumadzi; muja anakhala mumtendere unabala zipatso, wodzala ndi nthambi, chifukwa cha madzi ambiri.


Israele ndi mpesa wotambalala, wodzibalira wokha zipatso; monga umo zinachulukira zipatso zake, momwemo anachulukitsa maguwa a nsembe ake; monga mwa kukoma kwake kwa dziko lake anapanga zoimiritsa zokoma.


Tamvera tsono, Yoswa mkulu wa ansembe, iwe ndi anzako akukhala pansi pamaso pako; pakuti iwo ndiwo chizindikiro; pakuti taonani, ndidzafikitsa mtumiki wanga, ndiye Mphukira.


Koma Iye anayankha nati, Mmera wonse, umene Atate wanga wa Kumwamba sanaubzale, udzazulidwa.


Pakuti Ufumu wa Kumwamba ufanana ndi munthu mwini banja, amene anatuluka mamawa kukalembera antchito a m'munda wake wampesa.


Mverani fanizo lina: Panali munthu, mwini banja, amene analima munda wampesa, nauzunguniza linga, nakumba umo moponderamo mphesa, namanga nsanja, naukongoletsa kwa olima munda, namuka kwina.


Ndipo Iye anayamba kulankhula nao m'mafanizo. Munthu analima munda wampesa, nauzunguniza ndi linga, nakumba moponderamo mphesa, namanga nsanja, naukongoletsa kwa olima munda, namuka kwina.


Ndipo Iye ananena fanizo ili: Munthu wina anali ndi mkuyu wooka m'munda wake wampesa. Ndipo anadza nafuna chipatso pa uwu, koma anapeza palibe.


Chifukwa chilamulo chinapatsidwa mwa Mose; chisomo ndi choonadi zinadza mwa Yesu Khristu.


Uku ndiko kuunika kwenikweni, kumene kuunikira anthu onse akulowa m'dziko lapansi.


Nthambi iliyonse ya mwa Ine yosabala chipatso, aichotsa; ndi iliyonse yakubala chipatso, aisadza, kuti ikabale chipatso chochuluka.


Chifukwa chake Yesu anati kwa iwo, Indetu, indetu, ndinena kwa inu, Si Mose amene anakupatsani inu mkate wa Kumwamba; koma Atate wanga akupatsani inu mkate woona wa Kumwamba.


Pakuti thupi langa ndi chakudya ndithu, ndi mwazi wanga ndi chakumwa ndithu.


Koma ngati nthambi zina zinathyoledwa, ndipo iwe, ndiwe mtengo wa azitona wakuthengo, unalumikizidwa mwa izo, nugawana nazo za muzu za mafuta ake a mtengowo,


Pakuti ife ndife antchito anzake a Mulungu; chilimo cha Mulungu, chimango cha Mulungu ndi inu.


Ndikulemberaninso lamulo latsopano, ndicho chimene chili choona mwa Iye ndi mwa inu; kuti mdima ulinkupita, ndi kuunika koona kwayamba kuwala.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa