Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yohane 14:31 - Buku Lopatulika

31 koma kuti dziko lapansi lizindikire kuti ndikonda Atate, ndi kuti ndichita monga momwe Atate wandilamula. Nyamukani, tizimuka kuchokera kuno.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

31 koma kuti dziko lapansi lizindikire kuti ndikonda Atate, ndi kuti ndichita monga momwe Atate wandilamula. Nyamukani, tizimuka kuchokera kuno.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

31 koma anthu onse ayenera kudziŵa kuti ndimakonda Atate, nchifukwa chake ndikuchita monga Atate adandilamulira. Tiyeni, tizipita.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

31 koma kuti dziko lapansi lizindikire kuti Ine ndimakonda Atate ndi kuti ndimachita zokhazokha zimene Atate wandilamulira Ine. “Nyamukani; tizipita.”

Onani mutuwo Koperani




Yohane 14:31
17 Mawu Ofanana  

kuchita chikondwero chanu kundikonda, Mulungu wanga; ndipo malamulo anu ali m'kati mwamtima mwanga.


Ambuye Yehova watsegula khutu langa, ndipo sindinakhale wopanduka ngakhale kubwerera m'mbuyo.


Ndipo anamuka patsogolo pang'ono, nagwa nkhope yake pansi, napemphera, nati, Atate ngati nkutheka, chikho ichi chindipitirire Ine; koma si monga ndifuna Ine, koma Inu.


Ukani, timuke; taonani, iye wakundipereka wayandikira.


Koma ndili ndi ubatizo ndikabatizidwe nao; ndipo ndikanikizidwa Ine kufikira ukatsirizidwa!


Palibe wina andichotsera uwu, koma ndiutaya Ine ndekha. Ndili nayo mphamvu yakuutaya, ndi mphamvu ndili nayo yakuutenganso; lamulo ili ndinalandira kwa Atate wanga.


Moyo wanga wavutika tsopano; ndipo ndidzanena chiyani? Atate, ndipulumutseni Ine kunthawi iyi. Koma chifukwa cha ichi ndinadzera nthawi iyi.


Pakuti sindinalankhule mwa Ine ndekha; koma Atate wondituma Ine, yemweyu anandipatsa Ine lamulo, limene ndikanene, ndi limene ndikalankhule.


Koma pasanafike chikondwerero la Paska, Yesu, podziwa kuti nthawi yake idadza yakuchoka kutuluka m'dziko lino lapansi, kunka kwa Atate, m'mene anakonda ake a Iye yekha a m'dziko lapansi, anawakonda kufikira chimaliziro.


Monga momwe Atate wandikonda Ine, Inenso ndakonda inu; khalani m'chikondi changa.


Pamenepo Yesu anati kwa Petro, Longa lupanga m'chimake chake; chikho chimene Atate wandipatsa Ine sindimwere ichi kodi?


Yesu ananena nao, Chakudya changa ndicho kuti ndichite chifuniro cha Iye amene anandituma Ine, ndi kutsiriza ntchito yake.


ndipo popezedwa m'maonekedwe ngati munthu, anadzichepetsa yekha, nakhala womvera kufikira imfa, ndiyo imfa ya pamtanda.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa