Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 13:13 - Buku Lopatulika

13 Inu munditcha Ine Mphunzitsi, ndi Ambuye: ndipo munena bwino; pakuti ndine amene.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Inu munditcha Ine Mphunzitsi, ndi Ambuye: ndipo munena bwino; pakuti ndine amene.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Paja inu mumanditchula kuti, ‘Aphunzitsi’ ndiponso, ‘Ambuye.’ Apo mumalondola, pakuti ndine amene.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Inu mumanditcha Ine, ‘Mphunzitsi’ ndi ‘Mbuye,’ ndipo mumakhoza mukamatero, pakuti ichi ndi chimene Ine ndili.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 13:13
18 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova anati kwa ine, Waona bwino pakuti Ine ndidzadikira mau anga kuwachita.


monga Mwana wa Munthu sanadze kutumikiridwa koma kutumikira, ndi kupereka moyo wake dipo la anthu ambiri.


Ndipo anati kwa iye, Wayankha bwino; chita ichi, ndipo udzakhala ndi moyo.


Ndipo munditchuliranji Ine, Ambuye, Ambuye, ndi kusachita zimene ndizinena?


Simoni anayankha, nati, Ndiyesa kuti, iye amene anamkhululukira zoposa.


Koma ndiye Maria uja anadzoza Ambuye ndi mafuta onunkhira bwino, napukuta mapazi ake ndi tsitsi lake, amene mlongo wake Lazaro anadwala.


Ndipo m'mene anati ichi anachoka naitana Maria mbale wake m'tseri, ndi kuti, Wafika Mphunzitsi, akuitana iwe.


Pamenepo alongo ake anatumiza kwa Iye, nanena, Ambuye, onani, amene mumkonda adwala.


Chifukwa chake ndikuuzani inu, kuti palibe munthu wakulankhula mwa Mzimu wa Mulungu, anena, Yesu ngwotembereredwa; ndipo palibe wina akhoza kunena, Yesu ali Ambuye, koma mwa Mzimu Woyera.


koma kwa ife kuli Mulungu mmodzi, Atate amene zinthu zonse zichokera kwa Iye, ndi ife kufikira kwa Iye; ndi Ambuye mmodzi Yesu Khristu, amene zinthu zonse zili mwa Iye, ndi ife mwa Iye.


Ndipo, ambuye, inu, muwachitire zomwezo iwowa, nimuleke kuwaopsa; podziwa kuti Ambuye wao ndi wanu ali mu Mwamba, ndipo palibe tsankho kwa Iye.


ndi malilime onse avomere kuti Yesu Khristu ali Ambuye, kuchitira ulemu Mulungu Atate.


Komatu zenizeninso ndiyesa zonse zikhale chitayiko chifukwa cha mapambanidwe a chizindikiritso cha Khristu Yesu Ambuye wanga, chifukwa cha Iyeyu ndinatayikitsa zinthu zonse, ndipo ndiziyesa zapadzala, kuti ndikadzionjezere Khristu,


Ukhulupirira iwe kuti Mulungu ali mmodzi; uchita bwino; ziwanda zikhulupiriranso, ndipo zinthunthumira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa