Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 12:8 - Buku Lopatulika

8 Pakuti osauka muli nao pamodzi ndi inu nthawi zonse; koma simuli ndi Ine nthawi zonse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Pakuti osauka muli nao pamodzi ndi Ine nthawi zonse; koma simuli ndi Inu nthawi zonse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Pajatu osauka muli nawo nthaŵi zonse, koma Ine simudzakhala nane nthaŵi zonse.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Inu mudzakhala ndi osauka nthawi zonse, koma simudzakhala nane nthawi zonse.”

Onani mutuwo Koperani




Yohane 12:8
9 Mawu Ofanana  

Ndinamtsegulira bwenzi langalo; koma ndinampeza, bwenzi langa atachoka. Moyo wanga unalefuka polankhula iye: Ndinamfunafuna, osampeza; ndinamuitana, koma sanandivomere.


Pakuti nthawi zonse muli nao aumphawi pamodzi nanu; koma simuli ndi Ine nthawi zonse.


Pakuti muli nao aumphawi pamodzi ndi inu masiku onse, ndipo paliponse pamene mukafuna mukhoza kuwachitira zabwino; koma Ine simuli nane masiku onse.


Pamenepo Yesu anati kwa iwo, Katsala kanthawi kakang'ono ndipo kuunika kuli mwa inu. Yendani pokhala muli nako kuunika, kuti mdima sungakupezeni; ndipo woyenda mumdima sadziwa kumene amukako.


Tiana, katsala kanthawi ndikhala ndi inu. Mudzandifunafuna Ine; ndipo monga ndinanena kwa Ayuda, kuti kumene ndinkako Ine, inu simungathe kudza, momwemo ndinena kwa inu tsopano.


Pamenepo anatinso kwa iwo; Ndimuka Ine, ndipo mudzandifuna, ndipo m'tchimo lanu mudzafa: kumene ndimukako Ine, simudziwa kudza inu.


Popeza waumphawi salekana m'dziko, chifukwa chake ndikuuzani ndi kuti, Dzanja lanu mulitansire ndithu mbale wanu, ndi ozunzika anu, ndi aumphawi anu, a m'dziko mwanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa