Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 12:47 - Buku Lopatulika

47 Ndipo ngati wina akumva mau anga, ndi kusawasunga, Ine sindimweruza; pakuti sindinadze kudzaweruza dziko lapansi, koma kuti ndipulumutse dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

47 Ndipo ngati wina akumva mau anga, ndi kusawasunga, Ine sindimweruza; pakuti sindinadza kudzaweruza dziko lapansi, koma kuti ndipulumutse dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

47 Munthu akamva mau anga koma osaŵagwiritsa ntchito, Ine sindimzenga mlandu ai. Pakuti sindidadzere kudzazenga anthu mlandu, koma kudzaŵapulumutsa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

47 “Ndipo munthu amene amva mawu anga koma osawasunga, Ine sindimuweruza. Pakuti Ine sindinabwere kudzaweruza dziko lapansi, koma kudzapulumutsa.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 12:47
13 Mawu Ofanana  

Yang'anirani kuti musanyoze mmodzi wa ang'ono awa; pakuti ndinena kwa inu, kuti angelo ao apenya chipenyere nkhope ya Atate wanga wa Kumwamba.


monga Mwana wa Munthu sanadze kutumikiridwa koma kutumikira, ndi kupereka moyo wake dipo la anthu ambiri.


Pakuti Mwana wa Munthu anadza kufunafuna ndi kupulumutsa chotayikacho.


Ndipo anapita kumudzi kwina.


Iye amene akaniza Ine, ndi kusalandira mau anga, ali naye womweruza iye, mau amene ndalankhula, iwowa adzamweruza tsiku lomaliza.


Pakuti Mulungu sanatume Mwana wake kudziko lapansi, kuti akaweruze dziko lapansi, koma kuti dziko lapansi likapulumutsidwe ndi Iye.


Musayesa kuti Ine ndidzakunenezani inu kwa Atate; pali wakukunenezani, ndiye Mose, amene inu mumtama.


Ndili nazo zambiri zakulankhula ndi zakuweruza za inu; koma wondituma Ine ali woona; ndipo zimene ndazimva kwa Iye, zomwezo ndilankhula kwa dziko lapansi.


Ndipo yesani kulekerera kwa Ambuye wathu chipulumutso; monganso mbale wathu wokondedwa Paulo, monga mwa nzeru zopatsidwa kwa iye, anakulemberani;


Ndipo ife tapenyera, ndipo tichita umboni kuti Atate anatuma Mwana akhale Mpulumutsi wa dziko lapansi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa