Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yohane 12:46 - Buku Lopatulika

46 Ndadza Ine kuunika kudziko lapansi, kuti yense wokhulupirira Ine asakhale mumdima.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

46 Ndadza Ine kuunika kudziko lapansi, kuti yense wokhulupirira Ine asakhale mumdima.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

46 Ine ndine kuŵala, ndipo ndidadza pansi pano, kuti munthu aliyense wokhulupirira Ine, asamayende mu mdima.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

46 Ine ndabwera mʼdziko lapansi monga kuwunika, kotero palibe amene amakhulupirira Ine nʼkumakhalabe mu mdima.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 12:46
19 Mawu Ofanana  

Pakuti chitsime cha moyo chili ndi Inu, M'kuunika kwanu tidzaona kuunika.


Mutonthoze, mutonthoze mtima wa anthu anga, ati Mulungu wanu.


Ndidzapasula mapiri ndi zitunda, ndi kuumitsa zitsamba zao zonse; ndi kusandutsa nyanja zisumbu, ndi kuumitsa matamanda.


kuti utsegule maso akhungu, utulutse am'nsinga m'ndende, ndi iwo amene akhala mumdima, atuluke m'nyumba ya kaidi.


Koma inu akuopa dzina langa, dzuwa la chilungamo lidzakutulukirani, muli kuchiritsa m'mapiko mwake; ndipo mudzatuluka ndi kutumphatumpha ngati anaang'ombe onenepa otuluka m'khola.


anthu akukhala mumdima adaona kuwala kwakukulu, ndi kwa iwo okhala m'malo a mthunzi wa imfa, kuwala kunatulukira iwo.


kuunika kukhale chivumbulutso cha kwa anthu a mitundu, ndi ulemerero wa anthu anu Israele.


Uku ndiko kuunika kwenikweni, kumene kuunikira anthu onse akulowa m'dziko lapansi.


Koma chiweruziro ndi ichi, kuti kuunika kunadza kudziko lapansi, ndipo anthu anakonda mdima koposa kuunika; pakuti ntchito zao zinali zoipa.


Pamenepo Yesu analankhulanso nao, nanena, Ine ndine kuunika kwa dziko lapansi; iye wonditsata Ine sadzayenda mumdima, koma adzakhala nako kuunika kwa moyo.


Ndipo Yesu anati, Kudzaweruza ndadza Ine kudziko lino lapansi, kuti iwo osapenya apenye; ndi kuti iwo akupenya akhale osaona.


Pakukhala Ine m'dziko lapansi, ndili kuunika kwa dziko lapansi.


kukawatsegulira maso ao, kuti atembenuke kuchokera kumdima, kulinga kukuunika, ndi kuchokera ulamuliro wa Satana kulinga kwa Mulungu, kuti alandire iwo chikhululukiro cha machimo, ndi cholowa mwa iwo akuyeretsedwa ndi chikhulupiriro cha mwa Ine.


Mwa ichi anena, Khala maso wogona iwe, nuuke kwa akufa, ndipo Khristu adzawala pa iwe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa