Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 12:18 - Buku Lopatulika

18 Chifukwa cha ichinso khamulo linadza kudzakomana ndi Iye, chifukwa anamva kuti Iye adachita chizindikiro ichi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Chifukwa cha ichinso khamulo linadza kudzakomana ndi Iye, chifukwa anamva kuti Iye adachita chizindikiro ichi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Nchifukwa chake anthu onsewo adakamchingamira, popeza kuti anali atamva kuti Iye adaachita chizindikiro chozizwitsa chimenechi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Anthu ambiri, anapita kukakumana naye, chifukwa iwo anamva kuti Iye anachita chizindikiro chodabwitsachi.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 12:18
6 Mawu Ofanana  

Ndipo pakuyandikira Iye tsono potsetsereka pake paphiri la Azitona, unyinji wonse wa ophunzira anayamba kukondwera ndi kuyamika Mulungu ndi mau aakulu, chifukwa cha ntchito zonse zamphamvu anaziona;


pakuti ambiri a Ayuda anachoka chifukwa cha iye, nakhulupirira Yesu.


M'mawa mwake khamu lalikulu la anthu amene adadza kuchikondwerero, pakumva kuti Yesu alinkudza ku Yerusalemu,


Chifukwa chake Afarisi ananena wina ndi mnzake, Muona kuti simupindula kanthu konse; onani dziko litsata pambuyo pake pa Iye.


Chiyambi ichi cha zizindikiro zake Yesu anachita mu Kana wa mu Galileya naonetsera ulemerero wake; ndipo ophunzira ake anakhulupirira Iye.


Ndipo khamu lalikulu la anthu linamtsata Iye, chifukwa anaona zizindikiro zimene anachita pa odwala.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa