Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 11:32 - Buku Lopatulika

32 Pomwepo Maria, pofika pamene panali Yesu, m'mene anamuona Iye, anagwa pa mapazi ake, nanena ndi Iye, Ambuye, mukadakhala kuno Inu, mlongo wanga sakadamwalira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

32 Pomwepo Maria, pofika pamene panali Yesu, m'mene anamuona Iye, anagwa pa mapazi ake, nanena ndi Iye, Ambuye, mukadakhala kuno Inu, mlongo wanga sakadamwalira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

32 Maria atafika pamene panali Yesu, namuwona, adadzigwetsa kumapazi kwake nati, “Ambuye, mukadakhala kuno, sibwenzi mlongo wanga atamwalira.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

32 Mariya anafika pamalo pamene panali Yesu ndipo atamuona, anagwa pa mapazi ake ndipo anati, “Ambuye mukanakhala muli kuno mlongo wanga sakanamwalira.”

Onani mutuwo Koperani




Yohane 11:32
10 Mawu Ofanana  

ndipo anagwa nkhope yake pansi kumapazi ake, namyamika Iye; ndipo anali Msamariya ameneyo.


Koma Simoni Petro, pamene anaona, anagwa pansi pa mawondo ake a Yesu, nanena, Muchoke kwa ine, Ambuye, chifukwa ndine munthu wochimwa.


Ndipo onani, panadza munthu dzina lake Yairo, ndipo iye ndiye mkulu wa sunagoge; ndipo anagwa pamapazi ake a Yesu, nampempha Iye adze kunyumba kwake;


Koma ndiye Maria uja anadzoza Ambuye ndi mafuta onunkhira bwino, napukuta mapazi ake ndi tsitsi lake, amene mlongo wake Lazaro anadwala.


Ndipo Marita anati kwa Yesu, Ambuye, mukadakhala kuno mlongo wanga sakadafa.


Koma ena mwa iwo anati, Kodi uyu wotsegulira maso wosaona uja, sakanatha kodi kuchita kuti asafe ameneyunso?


Mkuluyo ananena kwa Iye, Ambuye, tsikani asanafe mwana wanga.


Ndipo ine Yohane ndine wakumva ndi wakupenya izi. Ndipo pamene ndinamva ndi kupenya, ndinagwa pansi kulambira pa mapazi a mngelo wakundionetsa izo.


Ndipo zamoyo zinai zinati, Amen. Ndipo akuluwo anagwa pansi nalambira.


Ndipo pamene adatenga bukulo, zamoyo zinai ndi akulu makumi awiri mphambu anai zinagwa pansi pamaso pa Mwanawankhosa, zonse zili nao azeze, ndi mbale zagolide zodzala ndi zofukiza, ndizo mapemphero a oyera mtima.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa