Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yohane 11:33 - Buku Lopatulika

33 Pamenepo Yesu, pakumuona iye alikulira, ndi Ayuda akumperekeza iye alikulira, anadzuma mumzimu, navutika mwini,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

33 Pamenepo Yesu, pakumuona iye alikulira, ndi Ayuda akumperekeza iye alikulira, anadzuma mumzimu, navutika mwini,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

33 Yesu ataona Maria akulira, ndiponso anthu amene adaadza naye iwonso akulira, zidamkhudza kwambiri ndipo adavutika mu mtima.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

33 Yesu ataona iye akulira, ndi Ayuda amene anabwera naye akuliranso, anakhudzidwa kwambiri ndi kuvutika mu mzimu.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 11:33
15 Mawu Ofanana  

Ndipo m'mene anawaunguza ndi mkwiyo, ndi kumva chisoni chifukwa cha kuuma kwa mitima yao, ananena kwa munthuyo, Tambasula dzanja lako. Ndipo analitambasula; ndipo linachira dzanja lake.


Ndipo Iye anawayankha nanena, Mbadwo wosakhulupirira inu, ndidzakhala ndi inu kufikira liti? Ndidzakulekererani nthawi yanji? Mudze naye kwa Ine.


koma ambiri a mwa Ayuda adadza kwa Marita ndi Maria, kudzawatonthoza mtima pa mlongo wao.


Pamenepo Ayuda okhala naye m'nyumba, ndi kumtonthoza iye, pakuona Maria ananyamuka msanga, natuluka, namtsata iye, ndi kuyesa kuti amuka kumanda kukalira komweko.


nati, Mwamuika iye kuti? Ananena ndi Iye, Ambuye, tiyeni mukaone.


Pamenepo Yesu, ndi kudzumanso mwa Iye yekha anadza kumanda. Koma panali phanga, ndipo mwala unaikidwa pamenepo.


Moyo wanga wavutika tsopano; ndipo ndidzanena chiyani? Atate, ndipulumutseni Ine kunthawi iyi. Koma chifukwa cha ichi ndinadzera nthawi iyi.


Yesu m'mene adanena izi, anavutika mumzimu, nachita umboni, nati, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, kuti mmodzi wa inu adzandipereka Ine.


Kondwani nao iwo akukondwera; lirani nao akulira.


Pakuti sitili naye mkulu wa ansembe wosatha kumva chifundo ndi zofooka zathu; koma wayesedwa m'zonse monga momwe ife, koma wopanda uchimo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa