Yohane 1:45 - Buku Lopatulika45 Filipo anapeza Natanaele, nanena naye, Iye amene Mose analembera za Iye m'chilamulo, ndi aneneri, tampeza, ndiye Yesu mwana wa Yosefe wa ku Nazarete. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201445 Filipo anapeza Natanaele, nanena naye, Iye amene Mose analembera za Iye m'chilamulo, ndi aneneri, tampeza, ndiye Yesu mwana wa Yosefe wa ku Nazarete. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa45 Filipo adakapeza Natanaele namuuza kuti, “Tampeza Ujayu amene Mose adalemba za Iye m'buku la Malamulo, uja anenerinso adalemba za Iye. Ndi Yesu Mwana wa Yosefe, wa ku Nazarete.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero45 Filipo anakapeza Natanieli ndipo anamuwuza kuti, “Ife tapeza amene Mose analemba za Iye mʼmalamulo, ndi zimene aneneri analembanso za Iye, Yesu wa ku Nazareti, mwana wa Yosefe.” Onani mutuwo |