Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 1:42 - Buku Lopatulika

42 Anadza naye kwa Yesu. M'mene anamyang'ana iye, anati, Uli Simoni mwana wa Yohane; udzatchedwa Kefa (ndiko kusandulika Petro).

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

42 Anadza naye kwa Yesu. M'mene anamyang'ana iye, anati, Uli Simoni mwana wa Yohane; udzatchedwa Kefa (ndiko kusandulika Petro).

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

42 Motero adamtenga kupita naye kwa Yesu. Pamene Yesu adamuwona adati, “Ndiwe Simoni, mwana wa Yohane. Dzina lako lidzakhala Kefa.” (Tanthauzo la Kefa ndi Petro, ndiye kuti Thanthwe.)

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

42 Kenaka iye anabweretsa Simoni kwa Yesu, amene anamuyangʼana ndipo anati, “Iwe ndiwe Simoni, mwana wa Yohane. Udzatchedwa Kefa” (limene litanthauza kuti Petro).

Onani mutuwo Koperani




Yohane 1:42
20 Mawu Ofanana  

Ndipo analowa wina, nauza mbuye wake, kuti, Buthulo lofuma ku dziko la Israele lanena zakutizakuti.


Ndipo maina ao a atumwiwo khumi ndi awiri ndi awa: woyamba Simoni wotchedwa Petro, ndi Andrea mbale wake; Yakobo mwana wa Zebedeo, ndi Yohane mbale wake;


Ndipo Simoni anamutcha Petro;


Koma Simoni Petro, pamene anaona, anagwa pansi pa mawondo ake a Yesu, nanena, Muchoke kwa ine, Ambuye, chifukwa ndine munthu wochimwa.


Simoni, amene anamutchanso Petro, ndi Andrea mbale wake, ndi Yakobo, ndi Yohane, ndi Filipo, ndi Bartolomeo,


Sindinena za inu nonse; ndidziwa amene ndawasankha: koma kuti cholemba chikwaniridwe, Iye wakudya mkate wanga anatsalimira pa Ine chidendene chake.


Anali pamodzi Simoni Petro, ndi Tomasi, wotchedwa Didimo, ndi Natanaele wa ku Kana wa ku Galileya, ndi ana a Zebedeo, ndi awiri ena a ophunzira ake.


Yesu ananena kwa iye, Muka, kamuitane mwamuna wako, nudze kuno.


Koma ichi ndinena, kuti yense wa inu anena, Ine ndine wa Paulo; koma ine wa Apolo; koma ine wa Kefa; koma ine wa Khristu.


ndi kuti anaonekera kwa Kefa; pamenepo kwa khumi ndi awiriwo;


ngati Paulo, kapena Apolo, kapena Kefa, kapena dziko lapansi, kapena moyo, kapena imfa, kapena za makono ano, kapena zilinkudza; zonse ndi zanu;


Kodi tilibe ulamuliro wakuyendayenda naye mkazi, ndiye mbale, monganso atumwi ena, ndi abale a Ambuye, ndi Kefa?


Pamenepo patapita zaka zitatu, ndinakwera kunka ku Yerusalemu kukazindikirana naye Kefa, ndipo ndinakhala kwa iye masiku khumi ndi asanu.


Koma pamene Kefa anadza ku Antiokeya ndinatsutsana naye pamaso pake, pakuti anatsutsika wolakwa.


ndipo pakuzindikira chisomocho chinapatsidwa kwa ine, Yakobo ndi Kefa ndi Yohane, amene anayesedwa mizati, anapatsa ine ndi Barnabasi dzanja lamanja la chiyanjano, kuti ife tipite kwa amitundu, ndi iwo kwa mdulidwe;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa