Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 1:31 - Buku Lopatulika

31 Ndipo sindinamdziwe Iye; koma kuti aonetsedwe kwa Israele, chifukwa cha ichi ndinadza ine kudzabatiza ndi madzi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

31 Ndipo sindinamdziwa Iye; koma kuti aonetsedwe kwa Israele, chifukwa cha ichi ndinadza ine kudzabatiza ndi madzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

31 Inenso sindinkamudziŵa, koma ndidabwera kudzabatiza ndi madzi kuti Aisraele amdziŵe.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

31 Ine mwini sindinamudziwe Iye, koma ndinabwera kubatiza ndi madzi kuti Iye adziwike mu Israeli.”

Onani mutuwo Koperani




Yohane 1:31
15 Mawu Ofanana  

Taonani, ndituma mthenga wanga, kuti akonzeretu njira pamaso panga; ndipo Ambuye amene mumfuna adzadza ku Kachisi wake modzidzimutsa; ndiye mthenga wa chipangano amene mukondwera naye; taonani akudza, ati Yehova wa makamu.


Pamenepo Yesu anachokera ku Galileya nadza ku Yordani kwa Yohane, kudzabatizidwa ndi iye.


nabatizidwa ndi iye mu mtsinjewo wa Yordani, alikuwulula machimo ao.


Ndipo adzamtsogolera Iye, ndi mzimu ndi mphamvu ya Eliya, kutembenuzira mitima ya atate kwa ana ao, ndi osamvera kuti atsate nzeru ya olungama mtima; kukonzeratu Ambuye anthu okonzeka.


Ndiye amene ndinati za Iye, Pambuyo panga palinkudza munthu amene analipo ndisanabadwe ine; pakuti anali woyamba wa ine.


Ndipo Yohane anachita umboni, nati, Ndinaona Mzimu alikutsika kuchokera Kumwamba monga nkhunda; nakhalabe pa Iye.


Ndipo sindinamdziwe Iye, koma wonditumayo kudzabatiza ndi madzi, Iyeyu ananena ndi ine, Amene udzaona Mzimu atsikira, nakhala pa Iye, yemweyu ndiye wakubatiza ndi Mzimu Woyera.


Iyeyu anadza mwa umboni kudzachita umboni za kuunikaku, kuti onse akakhulupirire mwa iye.


Ndipo anati Paulo, Yohane anabatiza ndi ubatizo wa kutembenuka mtima, nati kwa anthu, kuti amkhulupirire Iye amene adzadza pambuyo pake, ndiye Yesu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa