Yeremiya 8:6 - Buku Lopatulika6 Ndinatchera khutu, ndinamva koma sananene bwino; panalibe munthu amene anatembenuka kusiya zoipa zake, ndi kuti, Ndachita chiyani? Yense anatembenukira njira yake, monga akavalo athamangira m'nkhondo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20146 Ndinatchera khutu, ndinamva koma sananene bwino; panalibe munthu amene anatembenuka kusiya zoipa zake, ndi kuti, Ndachita chiyani? Yense anatembenukira njira yake, monga akavalo athamangira m'nkhondo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa6 Ndakhala ndikutchereza ndi kuŵamvetsera, koma sadalankhulepo zoona. Palibe wochimwa aliyense amene adandiwonetsa kuti walapa, namanena kuti, ‘Ndachitanji ine?’ Koma aliyense akungotsata njira zake, ngati kavalo wothamangira nkhondo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero6 Ine ndinatchera khutu kumvetsera koma iwo sanayankhulepo zoona. Palibe woyipa amene analapapo zoyipa zake, nʼkumati, ‘Ine ndachita chiyani?’ Aliyense akutsatira njira yake ngati kavalo wothamangira nkhondo. Onani mutuwo |