1 Nthawi yomweyo, ati Yehova, adzatulutsa m'manda mwao mafupa a mafumu a Yuda, ndi mafupa a akulu ake, ndi mafupa a ansembe, ndi mafupa a aneneri, ndi mafupa a okhala m'Yerusalemu,
1 Nthawi yomweyo, ati Yehova, adzatulutsa m'manda mwao mafupa a mafumu a Yuda, ndi mafupa a akulu ake, ndi mafupa a ansembe, ndi mafupa a aneneri, ndi mafupa a okhala m'Yerusalemu,
1 Chauta akunena kuti, “Pa nthaŵi imeneyo anthu adzatulutsa m'manda mafupa a akalonga, a ansembe, a aneneri ndiponso a anthu onse amene ankakhala ku Yerusalemu.
1 Yehova akuti, “ ‘Pa nthawi imeneyo, mafupa a mafumu ndi a akuluakulu a ku Yuda, mafupa a ansembe ndi a aneneri, ndiponso mafupa a anthu a ku Yerusalemu adzafukulidwa.
Ndipo iye anafuula mwa mau a Yehova kutemberera guwa la nsembe, nati, Guwa la nsembe, guwa la nsembe, atero Yehova, Taona mwana adzabadwa m'nyumba ya Davide, dzina lake ndi Yosiya, adzaphera pa iwe ngati nsembe anthu ansembe a misanje, amene alikufukiza zonunkhira pa iwe, nadzatentha pa iwe mafupa a anthu.
Pamenepo anaopa kwakukulu, popanda chifukwa cha kuopa, pakuti Mulungu anamwaza mafupa a iwo akuzinga iwe; unawachititsa manyazi, pakuti Mulungu anawakaniza.
Ndipo anthu amene adzanenera kwa inu adzaponyedwa kunja m'miseu ya Yerusalemu chifukwa cha chilala ndi lupanga; ndipo adzasowa akuwaika, ndi akazi ao, ndi ana ao aamuna ndi aakazi; ndipo ndidzatsanulira pa iwo zoipa zao.
Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Mowabu, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza anatentha mafupa a mfumu ya ku Edomu asanduke njereza;