Yeremiya 7:34 - Buku Lopatulika34 Ndipo ndidzaletsa m'mizinda ya Yuda, ndi m'miseu ya Yerusalemu, mau akukondwa ndi mau akusekera, ndi mau a mkwati ndi mau a mkwatibwi; pakuti dziko lidzasanduka bwinja. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201434 Ndipo ndidzaletsa m'midzi ya Yuda, ndi m'miseu ya Yerusalemu, mau akukondwa ndi mau akusekera, ndi mau a mkwati ndi mau a mkwatibwi; pakuti dziko lidzasanduka bwinja. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa34 Sikudzamvekanso mau achisangalalo ndi achimwemwe ku mizinda ya ku Yuda ndi ku miseu ya mu Yerusalemu. Sikudzamvekanso mau achikondwerero, a mkwati wamwamuna ndi wamkazi. Ndithudi dzikolo lidzasanduka chipululu.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero34 Ndidzathetsa nyimbo zonse zachisangalalo ndi zachikondwerero mʼmizinda ya ku Yuda ndi mʼmisewu ya ku Yerusalemu. Sikudzamvekanso mawu a chikondwerero a mkwatibwi ndi mkwati pakuti dzikolo lidzasanduka chipululu.” Onani mutuwo |
mudzamvekanso mau akukondwa ndi mau akusekera, mau a mkwati ndi mau a mkwatibwi, mau a iwo akuti, Myamikireni Yehova wa makamu, pakuti Yehova ndiye wabwino, chifundo chake nchosatha; ndi a iwo akutengera nsembe zoyamikira m'nyumba ya Yehova. Pakuti ndidzabweza undende wa dziko monga poyamba, ati Yehova.