Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 52:3 - Buku Lopatulika

3 Pakuti zonse zinachitika mu Yerusalemu ndi mu Yuda chifukwa cha mkwiyo wa Yehova, mpaka anawachotsa pamaso pake; ndipo Zedekiya anampandukira mfumu ya Babiloni.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Pakuti zonse zinachitika m'Yerusalemu ndi m'Yuda chifukwa cha mkwiyo wa Yehova, mpaka anawachotsa pamaso pake; ndipo Zedekiya anampandukira mfumu ya Babiloni.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Chifukwa cha zonse zimene zidachitika ku Yerusalemu ndi ku Yudazi, Chauta adakwiya kwambiri, mpaka kuŵachotsa anthuwo pamaso pake. Tsono Zedekiya adapandukira mfumu ya ku Babiloni.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Chifukwa cha zonse zimene zinachitika ku Yerusalemu ndi ku Yuda Yehova anakwiyira anthu ake mpaka kuwachotsa pamaso pake. Tsono Zedekiya anawukira mfumu ya ku Babuloni.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 52:3
19 Mawu Ofanana  

Taonani, mwandiingitsa ine lero lomwe padziko; ndi pankhope panu ndidzabisika; ndipo ndidzakhala wothawathawa ndi woyendayenda padziko lapansi; ndipo kudzatero kuti onse akundipeza adzandipha.


Ndipo Kaini anatuluka pamaso pa Yehova, ndipo anakhala m'dziko la Nodi, kum'mawa kwake kwa Edeni.


Ndipo mkwiyo wa Yehova unayakanso pa Israele, nafulumiza Davide pa iwo, nati, Muka, nuwerenge Israele ndi Yuda.


Wolemekezeka Yehova Mulungu wanu amene anakondwera nanu, kukuikani pa mpando wachifumu wa Israele; popeza Yehova anakonda Israele nthawi yosatha, chifukwa chake anakulongani inu ufumu, kuti muchite chiweruzo ndi chilungamo.


Chifukwa chake Yehova anakwiya naye Israele kwakukulu, nawachotsa pamaso pake osatsala mmodzi, koma fuko la Yuda lokha.


Ndipo Yehova anakaniza mbumba yonse ya Israele, nawazunza, nawapereka m'dzanja la ofunkha, mpaka anawataya pamaso pake.


mpaka Yehova adachotsa Israele pamaso pake, monga adanena mwa dzanja la atumiki ake onse aneneriwo. Momwemo Israele anachotsedwa m'dziko lao kunka nao ku Asiriya mpaka lero lino.


Pakuti mwa mkwiyo wa Yehova zonse zidachitika mu Yerusalemu ndi mu Yuda, mpaka adawataya pamaso pake; ndipo Zedekiya anapandukira mfumu ya Babiloni.


Ndiponso anapandukana naye mfumu Nebukadinezara, amene adamlumbiritsa pa Mulungu; koma anaumitsa khosi lake, nalimbitsa mtima wake kusatembenukira kwa Yehova Mulungu wa Israele.


kuti afunefune m'buku la chikumbutso la makolo anu; momwemo mudzapeza m'buku la chikumbutso, ndi kudziwa kuti mzinda uwu ndi mzinda wopanduka, ndi wosowetsa mafumu, ndi maiko; ndi kuti amadziyendera m'menemo kuyambira kale lomwe; ndicho chifukwa chakuti anapasula mzinda uwu.


Pochimwa dziko akalonga ake achuluka; koma anthu ozindikira ndi odziwa alikhazikikitsa nthawi yaikulu.


Tsoka kwa dzikowe, pamene mfumu yako ndiye mwana, ndipo akalonga ako adyera mamawa!


Ndipo ndidzapereka Ejipito m'manja mwa mbuye wankharwe; ndi mfumu yaukali idzawalamulira, ati Ambuye, Yehova wa makamu.


Ndipo onani, Ambuye, Yehova wa makamu, wachotsa ku Yerusalemu ndi ku Yuda mchirikizo wochirikiza chakudya chonse ndi madzi onse, zimene zinali mchirikizo;


Ine nditi, Uphungu wako, ndi mphamvu zako za kunkhondo, zingokhala mau achabe; tsopano ukhulupirira yani, kuti wandipandukira ine?


Ndipo Yehova anati kwa ine, Ngakhale Mose ndi Samuele akadaima pamaso panga, koma mtima wanga sukadasamalira anthu awa; muwachotse iwo pamaso panga, atuluke.


Ndipo ndidzakuchotsani inu pamaso panga, monga ndinachotsa abale anu onse, mbeu zonse za Efuremu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa