Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 42:2 - Buku Lopatulika

2 nati kwa Yeremiya mneneri, Chipembedzero chathu chigwe pamaso panu, nimutipempherere ife kwa Yehova Mulungu wanu, chifukwa cha otsala onsewa; pakuti tatsala ife owerengeka m'malo mwa ambiri, monga maso anu ationa ife;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 nati kwa Yeremiya mneneri, Chipembedzero chathu chigwe pamaso panu, nimutipempherere ife kwa Ambuye Mulungu wanu, chifukwa cha otsala onsewa; pakuti tatsala ife owerengeka m'malo mwa ambiri, monga maso anu ationa ife;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 “Ife tabwera ndi dandaulo lathu. Chonde, mutipempherere kwa Chauta, Mulungu wanu, ife amene tatsala oŵerengeka. Tangotsalatu ochepa chabe pa anthu ambiri, monga mukutiwoneramu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 kwa mneneri Yeremiya ndipo anamuwuza kuti, “Chonde imvani dandawulo lathu ndipo mutipempherere anthu otsalafe kwa Yehova Mulungu wanu. Pakuti monga tsopano mukuona, ngakhale kuti kale tinalipo ambiri, koma tsopano ochepa okha ndiye amene atsala.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 42:2
34 Mawu Ofanana  

Ndipo mfumu inayankha niti kwa munthu wa Mulungu, Undipembedzere Yehova Mulungu wako, nundipempherere, kuti dzanja langa libwerenso kwa ine. Ndipo munthuyo wa Mulungu anapembedza Yehova, ndipo dzanja la mfumu linabwezedwa kwa iye momwemo mwa kale.


Kupemba kwanga kudze pamaso panu; mundilanditse monga mwa mau anu.


Ndipo Farao anati, Ndidzakulolani mumuke, kuti mukamphere nsembe Yehova Mulungu wanu m'chipululu; komatu musamuke kutalitu: mundipembere.


Pembani kwa Yehova; chifukwa akwanira ndithu mabingu a Mulungu ndi matalala; ndipo ndidzakulolani mumuke, osakhalanso.


Ndipo pamene mutambasula manja anu, ndidzakubisirani inu maso anga; inde pochulukitsa mapemphero anu Ine sindidzamva; manja anu adzala mwazi.


Akadapanda Yehova wa makamu kutisiyira otsala ang'onong'ono ndithu, ife tikanakhala ngati Sodomu, ife tikadanga Gomora.


Kapena Yehova Mulungu wako adzamva mau a kazembeyo, amene mfumu ya Asiriya mbuyake inamtuma kukatonza Mulungu wamoyo, nadzadzudzula mau amene Yehova Mulungu wako adawamva; chifukwa chake, kweza pemphero lako chifukwa cha otsala osiyidwa.


Iwe waona zinthu zambiri, koma susamalira konse; makutu ako ali otseguka, koma sumva konse.


Yehova anati, Ndithu ndidzakulimbitsira iwe zabwino; ndithu ndidzapembedzetsa mdani kwa iwe nthawi ya zoipa ndi nthawi ya nsautso.


amene ati kwa mtengo, Iwe ndiwe atate wanga; ndi kwa mwala, Wandibala; pakuti anandipatsa Ine mbuyo, si nkhope yao; koma m'nthawi ya kuvutidwa kwao adzati, Ukani, tipulumutseni.


Tifunsirenitu ife kwa Yehova; pakuti Nebukadinezara mfumu wa ku Babiloni atithira ife nkhondo; kapena Yehova adzatichitira ife monga mwa ntchito zake zolapitsa, kuti atichokere.


Kapena pembedzero lao lidzagwa pamaso pa Yehova, ndipo adzabwerera yense kuleka njira yake yoipa; pakuti mkwiyo ndi ukali umene Yehova wanenera anthu awa ndi waukulu.


Tsopano tamvanitu, mbuyanga mfumu; pembedzero langa ligwe pamaso panu; kuti musandibwezere kunyumba ya Yonatani mlembi, ndingafe kumeneko.


Ndipo Zedekiya mfumu anatuma Yehukala mwana wa Selemiya, ndi Zefaniya mwana wa Maaseiya wansembe, kwa Yeremiya mneneri, kukanena, Mutipemphereretu kwa Yehova Mulungu wathu.


Ndipo mfumu Zedekiya anatuma, namtenga Yeremiya mneneri nalowa naye m'khomo lachitatu la nyumba ya Yehova; ndipo mfumu inati kwa Yeremiya, Ndidzakufunsa iwe kanthu; usandibisire ine kanthu.


Ndipo Yohanani mwana wa Kareya ananena kwa Gedaliya ku Mizipa m'tseri, kuti, Ndimuketu, ndikaphe Ismaele mwana wa Netaniya, anthu osadziwa; chifukwa chanji adzakuphani inu, kuti Ayuda onse amene anakusonkhanira inu amwazike, ndi otsala a Yuda aonongeke?


Pakuti mwanyenga m'miyoyo yanu; pakuti mwandituma ine kwa Yehova Mulungu wanu, ndi kuti, Mutipempherere ife kwa Yehova Mulungu wathu; ndipo monga mwa zonse Yehova Mulungu wathu adzanena, momwemo mutifotokozere ife; ndipo tidzachita.


Ha! Mzindawo unadzala anthu, ukhalatu pa wokha! Ukunga mkazi wamasiye! Waukuluwo mwa amitundu, kalonga wamkazi m'madera a dziko wasanduka wolamba!


Koma ndidzawasiya owerengeka apulumuke lupanga, ndi njala, ndi mliri, kuti afotokoze zonyansa zao kwa amitundu kumene afikako; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.


Inde angakhale alembera mwa amitundu ndidzawasonkhanitsa tsopano; ndipo ayamba kuchepa chifukwa cha katundu wa mfumu ya akalonga.


Popeza ndidzatumiza chilombo chakuthengo pakati pa inu, ndipo chidzalanda ana anu, ndi kuononga zoweta zanu ndipo chidzachepetsa inu kuti mukhale pang'ono; ndi njira zanu zidzakhala zakufa.


Ndipo kunachitika m'mene lidatha kudya msipu wa dziko, ndinati, Ambuye Yehova, khululukiranitu Yakobo; adzakhala chilili bwanji? Popeza ndiye wamng'ono.


Ndipo akadaleka kufupikitsidwa masiku awo, sakadapulumuka munthu aliyense: koma chifukwa cha osankhidwawo masiku awo adzafupikitsidwa.


Ndipo Simoni anayankha nati, Mundipempherere ine kwa Ambuye kuti zisandigwere izi mwanenazi.


Ndipo mudzatsala anthu pang'ono, mungakhale mudachuluka ngati nyenyezi za m'mwamba; popeza simunamvere mau a Yehova Mulungu wanu.


Ndipo kudzali kuti, monga Yehova anakondwera nanu kukuchitirani zabwino, ndi kukuchulukitsani; momwemo Yehova adzakondwera nanu kutayikitsa ndi kuononga inu, ndipo adzakuzulani kudziko kumene mulowako kulilandira.


Ndipo Yehova adzakubalalitsani mwa mitundu ya anthu, nimudzatsala pang'ono mwa amitundu, kumene Yehova adzakutsogolerani kwao.


Chifukwa chake muvomerezane wina ndi mnzake machimo anu, ndipo mupempherere wina kwa mnzake kuti muchiritsidwe. Pemphero la munthu wolungama likhoza kwakukulu m'machitidwe ake.


Ndipo anthu onse ananena ndi Samuele, Mupempherere akapolo anu kwa Yehova Mulungu wanu, kuti tingafe; popeza pamwamba pa zoipa zathu zonse tinaonjeza choipa ichi, chakuti tinadzipemphera mfumu.


Ndipo inenso, kukhale kutali ndi ine, kuchimwira Yehova ndi kuleka kukupemphererani; koma ndidzakulangizani njira yabwino ndi yolungama.


Ndipo ana a Israele anati kwa Samuele, Musaleke kutipempherera kwa Yehova Mulungu wathu, kuti Iye atipulumutse m'manja a Afilistiwo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa