Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 41:5 - Buku Lopatulika

5 anadza anthu ochokera ku Sekemu, ndi ku Silo, ndi ku Samariya, anthu makumi asanu ndi atatu, atameta ndevu zao, atang'amba zovala zao, atadzitematema, anatenga nsembe zaufa ndi lubani m'manja mwao, kunka nazo kunyumba ya Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 anadza anthu ochokera ku Sekemu, ndi ku Silo, ndi ku Samariya, anthu makamu asanu ndi atatu, atameta ndevu zao, atang'amba zovala zao, atadzitematema, anatenga nsembe zaufa ndi lubani m'manja mwao, kunka nazo kunyumba ya Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 kudafika anthu makumi asanu ndi atatu kuchokera ku Sekemu, ku Silo ndi ku Samariya. Ndevu zao adaameta, zovala zao zinali zong'ambikang'ambika, ndipo matupi ao anali otemekatemeka. Adatenga nsembe zaufa ndi lubani, kukapereka ku Nyumba ya Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 kunafika anthu 80 ochekera ku Sekemu, Silo ndi Samariya, amene anali atameta ndevu zawo, atangʼamba zovala zawo ndi kudzichekacheka. Iwowa anatenga chopereka cha ufa ndi lubani kuti adzapereke ku Nyumba ya Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 41:5
28 Mawu Ofanana  

Ndipo Yakobo anafika ndi mtendere kumzinda wa Sekemu umene uli m'dziko la Kanani, pamene anachokera ku Padanaramu; namanga tsasa pandunji pa mzindapo.


Pamene anamuona iye Sekemu, mwana wake wamwamuna wa Hamori Muhivi, kalonga wa dzikolo, anamtenga nagona ndi iye, namuipitsa.


Ndipo abale ake ananka kukaweta zoweta za atate wao mu Sekemu.


Chomwecho Hanuni anatenga anyamata a Davide nawameta ndevu zao mbali imodzi, nadula zovala zao pakati, kufikira m'matako ao, nawaleka amuke.


Ndipo Rehobowamu ananka ku Sekemu, popeza Aisraele onse anadza ku Sekemu kumlonga ufumu.


Ndipo Yerobowamu anamanga Sekemu m'mapiri a Efuremu, nakhalamo, natulukamo, namanga Penuwele.


Ndipo anagula kwa Semeri chitunda cha Samariya ndi matalente awiri a siliva, namanga pachitundapo, natcha dzina lake la mzinda anaumanga Samariya, monga mwa dzina la Semeri mwini chitundacho.


Ndipo chaka cha makumi atatu mphambu zisanu ndi zitatu cha Asa mfumu ya Yuda Ahabu mwana wa Omuri analowa ufumu wa Israele, nakhala Ahabu mwana wa Omuri mfumu ya Israele mu Samariya zaka makumi awiri mphambu ziwiri.


natentha nyumba ya Yehova, ndi nyumba ya mfumu, ndi nyumba zonse za mu Yerusalemu; ndi nyumba zonse zazikulu anazitentha ndi moto.


Ndipo Hanuni anatenga anyamata a Davide, nawameta, nadula malaya ao pakati kufikira m'matako, nawaleka achoke.


Pakuti atumiki anu akondwera nayo miyala yake, nachitira chifundo fumbi lake.


ndipo anachokera chokhalamo cha ku Silo, chihemacho adachimanga mwa anthu;


Akwera ku Kachisi, ndi ku Diboni, kumisanje, kukalira; pa Nebo ndi pa Medeba a Mowabu pali kulira; pamitu pao ponse pali dazi, ndevu zonse zametedwa.


Akulu ndi ang'onong'ono adzafa m'dziko muno; sadzaikidwa, anthu sadzachita maliro ao, sadzadzicheka, sadzadziyeseza adazi, chifukwa cha iwo;


Ndipo panali atapita masiku awiri atamupha Gedaliya, anthu osadziwa,


Dazi lafikira a Gaza; Asikeloni wathedwa, otsala m'chidikha chao; udzadzicheka masiku angati?


Pakuti mitu yonse ili yadazi, ndipo ndevu zili zometedwa; pa manja onse pali pochekedwachekedwa, ndi pachiuno chiguduli.


Koma pitani tsopano kumalo anga amene anali mu Silo, m'mene ndinaikamo dzina langa poyamba paja, ndi kuona chimene ndinachitira chifukwa cha zoipa za anthu anga Israele.


chifukwa chake ndidzaichitira nyumba iyi, imene itchedwa dzina langa, imene mukhulupirirayi, ndipo ndidzachitira malo amene ndinakupatsani inu ndi makolo anu, monga ndinachitira Silo.


ndipo ng'ambani mitima yanu, si zovala zanu ai; ndi kutembenukira kwa Yehova Mulungu wanu; pakuti Iye ndiye wachisomo, ndi wodzala chifundo, wosapsa mtima msanga, ndi wochuluka kukoma mtima, ndi woleka choipacho.


Inu ndinu ana a Yehova Mulungu wanu; musamadzicheka, kapena kumeta tsitsi pakati pamaso chifukwa cha akufa.


Ndipo msonkhano wonse wa ana a Israele unasonkhana ku Silo, nuutsa komweko chihema chokomanako; ndipo dziko linawagonjera.


Ndipo mafupa a Yosefe amene ana a Israele anakwera nao kuchokera ku Ejipito anawaika ku Sekemu, pa kadziko kamene adakagula Yakobo kwa ana a Hamori atate wa Sekemu ndi kuwapatsa ndalama zana; ndipo anakhala cholowa cha ana a Yosefe.


Motero anadziikira fano losema la Mika, limene adalipanga, masiku onse okhala nyumba ya Mulungu ku Silo.


Koma Abimeleki mwana wa Yerubaala anamuka ku Sekemu kwa abale a amai wake, nanena nao, ndi kwa banja lonse la nyumba ya atate wa amai wake, ndi kuti,


Ndipo popeza munthuyo adatero chaka ndi chaka, popita mkaziyo kunyumba ya Yehova, mnzakeyo amamputa; chifukwa chake iye analira misozi, nakana kudya.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa