Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 40:9 - Buku Lopatulika

9 Ndipo Gedaliya mwana wa Ahikamu mwana wa Safani anawalumbirira iwo ndi anthu ao, kuti, Musaope kuwatumikira Ababiloni; khalani m'dzikomu, mutumikire mfumu ya ku Babiloni, ndipo kudzakukomerani.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo Gedaliya mwana wa Ahikamu mwana wa Safani anawalumbirira iwo ndi anthu ao, kuti, Musaope kuwatumikira Ababiloni; khalani m'dzikomu, mutumikire mfumu ya ku Babiloni, ndipo kudzakukomerani.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Onsewo, Gedaliya mwana wa Ahikamu, mdzukulu wa Safani, adaŵalonjeza molumbira kuti, “Musaope kuŵagwirira ntchito Ababiloniwo. Khalani m'dzikomu, muzimera mfumu ya ku Babiloni, ndipo zinthu zonse zidzakuyenderani bwino.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Gedaliya mwana wa Ahikamu, mdzukulu wa Safani, anawalonjeza iwo pamodzi ndi anthuwo mwalumbiro. Ndipo anati, “Musaope kuwatumikira Ababuloni. Khalani mʼdziko muno, tumikirani mfumu ya ku Babuloni, ndipo zinthu zidzakuyenderani bwino.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 40:9
9 Mawu Ofanana  

Ndipo anaona popumulapo kuti panali pabwino, ndi dziko kuti linali lokondweretsa; ndipo anaweramitsa phewa lake kuti anyamule, nakhala kapolo wakugwira ntchito ya msonkho.


Nawalumbirira Gedaliya iwo ndi anthu ao, nanena nao, Musamaopa anyamata a Ababiloni; khalani m'dziko; tumikirani mfumu ya Babiloni, ndipo kudzakukomerani.


Pakuti udzadya za ntchito ya manja ako; wodala iwe, ndipo kudzakukomera.


Khulupirira Yehova, ndipo chita chokoma; khala m'dziko, ndipo tsata choonadi.


Koma mtundu umene udzaika khosi lao pansi pa goli la mfumu ya ku Babiloni, ndi kumtumikira iye, mtundu umene ndidzaulola ukhalebe m'dziko lao, ati Yehova; ndipo adzalilima, nadzakhala momwemo.


Ha! Mzindawo unadzala anthu, ukhalatu pa wokha! Ukunga mkazi wamasiye! Waukuluwo mwa amitundu, kalonga wamkazi m'madera a dziko wasanduka wolamba!


Timalowa m'zoopsa potenga zakudya zathu, chifukwa cha lupanga la m'chipululu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa