Yeremiya 40:10 - Buku Lopatulika10 Koma ine, taonani, ndidzakhala pa Mizipa, ndiima pamaso pa Ababiloni, amene adzadza kwa ife; koma inu sonkhanitsani vinyo ndi zipatso zamalimwe ndi mafuta, muziike m'mbiya zanu, nimukhale m'mizinda imene mwailanda. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201410 Koma ine, taonani, ndidzakhala pa Mizipa, ndiima pamaso pa Ababiloni, amene adzadza kwa ife; koma inu sonkhanitsani vinyo ndi zipatso zamalimwe ndi mafuta, muziike m'mbiya zanu, nimukhale m'midzi imene mwailanda. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa10 Ine nditsalira ku Mizipa kuti ndizikuimirirani kwa Ababiloni akamabwera. Koma inu mutenge zipatso zanu, vinyo wanu, mafuta anu, ndipo muzisunge ndithu. Muzikhala m'mizinda imene mwalandayo.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero10 Ine ndidzakhala ku Mizipa kuti ndizikuyimirirani kwa Ababuloni amene azidzabwera kwa ife, koma inu muzikolola vinyo wanu, zipatso zanu, mafuta anu ndi kuzisunga mʼmitsuko yanu, nʼkumakhala mʼmizinda imene mwalandayo.” Onani mutuwo |