Yeremiya 40:7 - Buku Lopatulika7 Ndipo pamene akulu onse a makamu amene anali m'minda, iwo ndi anthu ao, anamva kuti mfumu ya ku Babiloni adamuika Gedaliya mwana wa Ahikamu wolamulira dziko, nampatsira amuna, ndi akazi, ndi ana, ndi aumphawi a m'dzikomo, a iwo amene sanatengedwe ndende kunka nao ku Babiloni; Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20147 Ndipo pamene akulu onse a makamu amene anali m'minda, iwo ndi anthu ao, anamva kuti mfumu ya ku Babiloni adamuika Gedaliya mwana wa Ahikamu wolamulira dziko, nampatsira amuna, ndi akazi, ndi ana, ndi aumphawi a m'dzikomo, a iwo amene sanatengedwe ndende kunka nao ku Babiloni; Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa7 Panali atsogoleri ena ankhondo amene sadadzipereke nao. Iwowo pamodzi ndi anthu ao adamva kuti mfumu ya ku Babiloni idaika Gedaliya, mwana wa Ahikamu, kuti akhale bwanamkubwa wa dzikolo, aziyang'anira anthu osauka kwambiri aja, amuna, akazi ndi ana, amene sadaŵatenge ukapolo kupita nawo ku Babiloni. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero7 Panali atsogoleri ena a nkhondo ndi anthu awo amene sanadzipereke nawo. Iwowa anamva kuti mfumu ya ku Babuloni inasankha Gedaliya mwana wa Ahikamu kukhala bwanamkubwa wa dzikolo ndipo kuti yamuyika kukhala wolamulira amuna, akazi ndi ana amene anali osauka kwambiri mʼdzikomo, amene sanawagwire ukapolo kupita nawo ku Babuloni. Onani mutuwo |