Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 32:3 - Buku Lopatulika

3 Pakuti Zedekiya mfumu ya Yuda inamtsekera iye, nati, Chifukwa chanji ulinkunenera, kuti, Yehova atero, Taonani, ndidzapereka mzinda uwu m'dzanja la mfumu ya Babiloni, ndipo iye adzaulanda,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Pakuti Zedekiya mfumu ya Yuda inamtsekera iye, nati, Chifukwa chanji ulinkunenera, kuti, Yehova atero, Taonani, ndidzapereka mudzi uwu m'dzanja la mfumu ya Babiloni, ndipo iye adzaulanda,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Zedekiya mfumu ya ku Yuda ndiye amene adaamtsekera m'menemo. Mfumuyo idaamufunsa kuti, “Chifukwa chiyani iwe ukulosa zakuti, Chauta akunena kuti, ‘Mzindawu ndidzaupereka kwa mfumu ya ku Babiloni, ndipo adzaulanda.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Tsono Zedekiya mfumu ya Yuda nʼkuti itamutsekera mʼmenemo, ndipo inati, “Nʼchifukwa chiyani ukulosera motero? Iwe ukunena kuti, ‘Yehova akuti: Ndidzapereka mzinda uno kwa mfumu ya ku Babuloni, ndipo idzawulanda.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 32:3
23 Mawu Ofanana  

Ndipo nthawi ya nsautso yake anaonjeza kulakwira Yehova, mfumu Ahazi yemweyo.


Ndipo mfumu ya Aejipito inanena nao, Inu, Mose ndi Aroni, chifukwa ninji mumasulira anthu ntchito zao? Mukani ku akatundu anu.


Ndapanda ana anu mwachabe; sanamvere kulanga; lupanga lanu ladya aneneri anu, monga mkango wakuononga.


Ndipo Yeremiya anati kwa iwo, Muzitero kwa Zedekiya:


Ndipo padzakhala, kuti mtundu ndi ufumu umene sudzamtumikira Nebukadinezara yemweyo mfumu ya ku Babiloni, mtundu umenewo Ine ndidzalanga, ati Yehova, ndi lupanga, ndi njala, ndi mliri, mpaka nditatha onse ndi dzanja lake.


Ndipo Zedekiya mfumu ya Yuda ndi akulu ake ndidzawapereka m'dzanja la adani ao, ndi m'dzanja la akufuna moyo wao, ndi m'dzanja la nkhondo ya mfumu ya ku Babiloni, imene yakuchokerani.


Ndipo za Yehoyakimu mfumu ya Yuda uziti, Yehova atero: Iwe watentha mpukutu uwu, ndi kuti, Bwanji walemba m'menemo, kuti, Mfumu ya ku Babiloni idzadzadi nidzaononga dziko ili, nidzatha m'menemo anthu ndi nyama?


Ndipo Yeremiya analikuyendayenda mwa anthu; chifukwa sanamuike iye m'nyumba yandende.


koma ngati simudzatulukira kwa akulu a mfumu ya ku Babiloni, mzindawu udzaperekedwa m'dzanja la Ababiloni, ndipo udzatenthedwa ndi moto, ndipo simudzapulumuka m'manja mwao.


Yehova atero, Mzindawu udzapatsidwatu m'dzanja la nkhondo ya mfumu ya ku Babiloni, ndipo adzaulanda.


Ndipo akulu anati kwa mfumu, Munthu uyu aphedwetu; chifukwa analopetsa manja a anthu a nkhondo otsala m'mzinda muno, ndi manja a anthu onse, pakunena kwa iwo mau otero; pakuti munthu uyu safuna mtendere wa anthu awa, koma nsautso yao.


Ebedemeleki anatuluka m'nyumba ya mfumu, nanena ndi mfumu, kuti,


Yehova Inu, maso anu sali pachoonadi kodi? Munawapanda iwo, koma sanaphwetekedwe mtima; munawatha iwo, koma akana kudzudzulidwa; alimbitsa nkhope zao koposa mwala; akana kubwera.


Goli la zolakwa zanga lamangidwa ndi dzanja lake; zalukidwa, zakwera pakhosi panga; iye wakhumudwitsa mphamvu yanga; Ambuye wandipereka m'manja mwao, sindithai kuwagonjetsa.


koma usaneneranso ku Betele; pakuti pamenepo mpamalo opatulika a mfumu, ndiyo nyumba yachifumu.


ndipo anati, nanena naye, Mutiuze muchita izi ndi ulamuliro wotani? Kapena ndani iye amene anakupatsani ulamuliro umene?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa