Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 32:2 - Buku Lopatulika

2 Nthawi yomweyo nkhondo ya mfumu ya Babiloni inamangira Yerusalemu misasa; ndipo Yeremiya mneneri anatsekeredwa m'bwalo la kaidi, linali kunyumba ya mfumu ya Yuda.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Nthawi yomweyo nkhondo ya mfumu ya Babiloni inamangira Yerusalemu misasa; ndipo Yeremiya mneneri anatsekeredwa m'bwalo la kaidi, linali kunyumba ya mfumu ya Yuda.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Pa nthaŵi imeneyo ankhondo a mfumu ya ku Babiloni ankazinga Yerusalemu ndi zithando zankhondo. Mneneri Yeremiya anali atamtsekera m'bwalo la alonda, m'kati mwa nyumba yaufumu ya ku Yuda.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Pa nthawi imeneyi nʼkuti ankhondo a mfumu ya ku Babuloni atazinga Yerusalemu, ndipo mneneri Yeremiya ndiye anamutsekera mʼbwalo la alonda mʼnyumba yaufumu ya ku Yuda.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 32:2
15 Mawu Ofanana  

Ndipo kunali chaka chachisanu ndi chinai cha ufumu wake, mwezi wakhumi, tsiku lakhumi la mwezi, Nebukadinezara mfumu ya Babiloni, iye ndi khamu lake lonse anadzera Yerusalemu, naumangira misasa, naumangira timalinga mouzinga.


Palali mwana wa Uzai anakonza pandunji popindirira, ndi nsanja yosomphoka pa nyumba ya mfumu ya kumtunda, imene ili kubwalo la kaidi. Potsatizana naye anakonza Pedaya mwana wa Parosi.


Munandisiyanitsira wodziwana nane kutali; munandiika ndiwakhalire chonyansa. Ananditsekereza, osakhoza kutuluka ine.


Pakuti Zedekiya mfumu ya Yuda inamtsekera iye, nati, Chifukwa chanji ulinkunenera, kuti, Yehova atero, Taonani, ndidzapereka mzinda uwu m'dzanja la mfumu ya Babiloni, ndipo iye adzaulanda,


Ndipo Hanamele mwana wa mbale wa atate wanga anadza kwa ine m'bwalo la kaidi monga mwa mau a Yehova, nati kwa ine, Gulatu munda wanga, wa ku Anatoti, m'dziko la Benjamini; pakuti mphamvu yakulowa ndi yakuombola ndi yako; udzigulire wekha. Pamenepo ndinadziwa kuti awa ndi mau a Yehova.


Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yeremiya nthawi yachiwiri, pamene iye anali chitsekedwere m'bwalo la kaidi, kuti,


Mau amene anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova, pamene Nebukadinezara mfumu ya Babiloni, ndi nkhondo yake yonse, ndi maufumu onse a dziko lapansi amene anagwira mwendo wake, ndi anthu onse, anamenyana ndi Yerusalemu, ndi mizinda yake yonse, akuti,


Ndipo Yeremiya anauza Baruki, kuti, Ndaletsedwa sindithai kulowa m'nyumba ya Yehova;


Ndipo akulu anakwiyira Yeremiya, nampanda iye, namuika m'nyumba yandende m'nyumba ya Yonatani mlembi; pakuti anaiyesa ndende.


Ndipo Zedekiya mfumu analamula, ndipo anamuika Yeremiya m'bwalo la kaidi, tsiku ndi tsiku, nampatsa mkate wofuma kumseu wa oumba mikate, mpaka unatha mkate wonse wa m'mzinda. Ndipo Yeremiya anakhala m'bwalo la kaidi.


Ndipo Yeremiya analikuyendayenda mwa anthu; chifukwa sanamuike iye m'nyumba yandende.


Ndipo anamkweza Yeremiya ndi zingwe, namtulutsa m'dzenjemo; ndipo Yeremiya anakhalabe m'bwalo la kaidi.


Ndipo anatenga Yeremiya, namponya iye m'dzenje la Malikiya mwana wake wa mfumu, limene linali m'bwalo la kaidi; ndipo anamtsitsa Yeremiya ndi zingwe. Koma m'dzenjemo munalibe madzi, koma thope; namira Yeremiya m'thopemo.


Sekerani, sangalalani: chifukwa mphotho yanu ndi yaikulu mu Mwamba: pakuti potero anazunza aneneri anakhalawo musanabadwe inu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa