Yeremiya 30:3 - Buku Lopatulika3 Pakuti, taona, masiku adzadza, ati Yehova, amene ndidzabwezanso undende wa anthu anga Aisraele ndi Ayuda, ati Yehova; ndipo ndidzawabwezera kudziko limene ndinapatsa makolo ao. Ndipo adzakhala nalo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20143 Pakuti, taona, masiku adzadza, ati Yehova, amene ndidzabwezanso undende wa anthu anga Aisraele ndi Ayuda, ati Yehova; ndipo ndidzawabwezera kudziko limene ndinapatsa makolo ao. Ndipo adzakhala nalo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa3 Nthaŵi ikubwera yoti ndidzaŵabwezere anthu anga, Israele ndi Yuda, ku dziko limene ndidapatsa makolo ao, ndipo lidzakhaladi lao.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero3 Nthawi ikubwera pamene ndidzachotse anthu anga, Israeli ndi Yuda kuchokera ku ukapolo ndi kuwabwezera dziko limene ndinapatsa makolo awo,’ akutero Yehova.” Onani mutuwo |
Chaka chachiwiri tsono chakufika iwo kunyumba ya Mulungu ku Yerusalemu, mwezi wachiwiri, Zerubabele mwana wa Sealatiele, ndi Yesuwa mwana wa Yozadaki, ndi abale ao otsala, ansembe ndi Alevi, ndi onse ochokera kundende kudza ku Yerusalemu, anayamba, naika Alevi a zaka makumi awiri ndi mphambu, ayang'anire ntchito ya nyumba ya Yehova.
Anthu adzagula minda ndi ndalama, adzalembera makalata ogulira, adzawasindikiza, adzaitana mboni, m'dziko la Benjamini, ndi m'malo ozungulira Yerusalemu, ndi m'mizinda ya Yuda, ndi m'mizinda ya kumtunda, ndi m'mizinda ya kuchidikha, ndi m'mizinda ya kumwera; pakuti ndidzabweza undende wao, ati Yehova.