Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 3:11 - Buku Lopatulika

11 Ndipo Yehova anati kwa ine, Israele wobwerera anadzionetsa wolungama kopambana ndi Yuda wonyenga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Ndipo Yehova anati kwa ine, Israele wobwerera anadzionetsa wolungama kopambana ndi Yuda wonyenga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Chauta adandiwuzanso kuti, “Israele wosakhulupirika uja kupalamula kwake nkochepa, kuyerekeza ndi Yuda wosakhulupirika uja.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Yehova anandiwuza kuti, “Kusakhulupirika kwa Israeli nʼkochepa kuyerekeza ndi kusakhulupirika kwa Yuda.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 3:11
9 Mawu Ofanana  

Abwerera kuchitanso zoipa za makolo ao, amene anakana kumva mau anga; ndipo atsata milungu ina kuti aitumikire; nyumba ya Israele ndi nyumba ya Yuda zaswa pangano langa limene ndinapangana ndi makolo ao.


Bwerani, ana inu obwerera, ndidzachiritsa mabwerero anu. Taonani, tadza kwa Inu; pakuti ndinu Yehova Mulungu wathu.


Ndipo ndinati atachita zimenezo zonse, Adzabwera kwa Ine; koma sanabwere, ndipo mphwake wonyenga, Yuda, anaona.


Ndipo ndinaona, kuti, ndingakhale ndikamchotsa Israele wobwerera m'mbuyo, ndi kumpatsa kalata yachilekaniro chifukwa cha kuchita chigololo iye, mphwake Yuda wonyenga sanaope, koma iye yemwe ananka nachita dama.


Koma sunayende m'njira zao, kapena kuchita monga mwa zonyansa zao pang'ono pokha; unawaposa iwo m'kuvunda kwako, m'njira zako zonse.


Pamene mng'ono wake Oholiba anachiona, anavunda ndi kuumirira kwake koposa iyeyo; ndi zigololo zake zidaposa zigololo za mkulu wake.


Ndipo anthu anga alimbika kubwerera m'mbuyo kundileka Ine; chinkana akawaitana atsate Iye ali m'mwamba, sadzakweza ndi mmodzi yense.


Pakuti Israele wachita kuuma khosi ngati ng'ombe yaikazi yaing'ono youma khosi; tsopano Yehova adzawadyetsa ngati mwanawankhosa kuthengo lalikulu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa