Yeremiya 27:8 - Buku Lopatulika8 Ndipo padzakhala, kuti mtundu ndi ufumu umene sudzamtumikira Nebukadinezara yemweyo mfumu ya ku Babiloni, mtundu umenewo Ine ndidzalanga, ati Yehova, ndi lupanga, ndi njala, ndi mliri, mpaka nditatha onse ndi dzanja lake. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20148 Ndipo padzakhala, kuti mtundu ndi ufumu umene sudzamtumikira Nebukadinezara yemweyo mfumu ya ku Babiloni, mtundu umenewo Ine ndidzalanga, ati Yehova, ndi lupanga, ndi njala, ndi chaola, mpaka nditatha onse ndi dzanja lake. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa8 “Koma ngati anthu a mtundu wina uliwonse kapena a dziko lina lililonse adzakana kutumikira Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, kapena kugonjera ulamuliro wake, Ineyo ndidzaŵalanga ndi nkhondo, njala ndi mliri, mpaka nditaŵapereka m'manja mwake kotheratu,” akuterotu Chauta. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero8 “ ‘Koma ngati anthu a mtundu wina uliwonse kapena ufumu wina uliwonse adzakana kutumikira Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni kapena kusenza goli lake, Ine ndidzalanga mtundu umenewo ndi lupanga, ndi njala ndi mliri, akutero Yehova, mpaka nditawapereka mʼmanja mwake kotheratu. Onani mutuwo |
taonani, Ine, ndidzatuma ndi kutenga mabanja onse a kumpoto, ati Yehova, ndipo ndidzatuma kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, mtumiki wanga, ndipo ndidzatengera iwo padziko lino, ndi pa okhalamo ake onse, ndi pa mitundu iyi yozungulira, ndipo ndidzathetsa iwo ndithu, ndi kuwayesa iwo chizizwitso, ndi chotsonyetsa, ndi bwinja lamuyaya.