Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 27:2 - Buku Lopatulika

2 Yehova atero kwa ine: Udzipangire zomangira ndi magoli, nuziike pakhosi pako;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Yehova atero kwa ine: Udzipangire zomangira ndi magoli, nuziike pakhosi pako;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 “Tenga nsinga zachikopa ndi mitengo ya goli, uzimange m'khosi mwako.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 “Tenga zingwe zomangira ndi mitengo ya goli ndipo uzimangirire mʼkhosi mwako.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 27:2
18 Mawu Ofanana  

Ndipo Zedekiya mwana wa Kenana anadzisulira nyanga zachitsulo, nati, Atero Yehova, Ndi izi mudzagunda nazo Aaramu mpaka atatha psiti.


Edomu, ndi Mowabu, ndi ana a Amoni,


Koma mtundu umene udzaika khosi lao pansi pa goli la mfumu ya ku Babiloni, ndi kumtumikira iye, mtundu umene ndidzaulola ukhalebe m'dziko lao, ati Yehova; ndipo adzalilima, nadzakhala momwemo.


Ndipo ndinanena kwa Zedekiya mfumu ya Yuda monga mau onse amenewa, kuti, Longani makosi anu m'goli la mfumu ya ku Babiloni, ndi kumtumikira iye ndi anthu ake, ndipo mudzakhala ndi moyo.


Pakuti padzakhala tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu, kuti ndidzathyola goli lake pakhosi pako, ndipo ndidzadula zomangira zako; ndipo alendo sadzamuyesanso iye mtumiki wao;


Ndi ku Tehafinehesi kudzada usana, pakuthyola Ine magoli a Ejipito komweko; ndi mphamvu yake yodzikuza idzalekeka m'menemo; kunena za ilo mtambo udzaliphimba, ndi ana ake aakazi adzalowa undende.


Sula unyolo, popeza dziko ladzala ndi milandu yamwazi, ndi mzinda wadzala ndi chiwawa.


Ambuye Yehova anandionetsa chotere; ndipo taonani, anaumba dzombe, poyamba kuphuka kwa udzu wa chibwereza; ndipo taonani, ndicho chibwereza atawusengera mfumu.


Ambuye Yehova anandionetsa chotere; ndipo taonani, Ambuye Yehova anaitana kuti atsutse ndi moto; ndipo unanyambita chakuya chachikulu ukadanyambitanso dziko.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa