Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 26:9 - Buku Lopatulika

9 Bwanji mwanenera m'dzina la Yehova, kuti, Nyumba iyi idzafanana ndi Silo, mzinda uwu udzakhala bwinja lopanda wokhalamo? Ndipo anthu onse anamsonkhanira Yeremiya m'nyumba ya Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Bwanji mwanenera m'dzina la Yehova, kuti, Nyumba iyi idzafanana ndi Silo, mudzi uwu udzakhala bwinja lopanda wokhalamo? Ndipo anthu onse anamsonkhanira Yeremiya m'nyumba ya Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Chifukwa chiyani walosa m'dzina la Chauta kuti Nyumba ino idzaonongedwa ngati Silo, ndipo kuti mzinda uno udzasanduka wopanda anthu, ngati chipululu?” Motero anthu onse adasonkhana nazinga Yeremiya m'Nyumba ya Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Chifukwa chiyani walosera mʼdzina la Yehova kuti Nyumba ino idzakhala ngati Silo ndipo mzinda uno udzakhala wopanda anthu ngati chipululu?” Anthu onse anamuzungulira Yeremiya mʼNyumba ya Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 26:9
28 Mawu Ofanana  

Ndipo kunali, pakulankhula naye mfumu, inanena naye, Takuika kodi ukhale wopangira mfumu? Leka, angakukanthe. Pamenepo mneneriyo analeka, nati, Ndidziwa kuti Mulungu watsimikiza mtima kukuonongani, popeza mwachita ichi ndi kusamvera kupangira kwanga.


amene apalamulitsa munthu mlandu, namtchera msampha iye amene adzudzula pachipata, nambweza wolungama ndi chinthu chachabe.


Pakuti Zedekiya mfumu ya Yuda inamtsekera iye, nati, Chifukwa chanji ulinkunenera, kuti, Yehova atero, Taonani, ndidzapereka mzinda uwu m'dzanja la mfumu ya Babiloni, ndipo iye adzaulanda,


Atero Yehova: M'malo muno, m'mene muti, Ndi bwinja, mopanda munthu, mopanda nyama, m'mizinda ya Yuda, m'makwalala a Yerusalemu, amene ali bwinja, opanda munthu, opanda wokhalamo, opanda nyama,


Ndipo za Yehoyakimu mfumu ya Yuda uziti, Yehova atero: Iwe watentha mpukutu uwu, ndi kuti, Bwanji walemba m'menemo, kuti, Mfumu ya ku Babiloni idzadzadi nidzaononga dziko ili, nidzatha m'menemo anthu ndi nyama?


Ndipo ndidzayesa Yerusalemu miyulu, mbuto ya ankhandwe; ndipo ndidzayesa mizinda ya Yuda bwinja, lopanda wokhalamo.


Ndicho chifukwa cha machimo a aneneri ndi mphulupulu za ansembe ake, amene anakhetsa mwazi wa olungama pakati pake.


Iwo adana naye wodzudzula kuchipata, nanyansidwa naye wolunjikitsa mau.


Musamanenera, amanenera ati. Sadzanenera kwa awa; matonzo sadzachoka.


Ndipo m'mene Iye analowa mu Kachisi, ansembe aakulu ndi akulu a anthu anadza kwa Iye analikuphunzitsa, nanena, Muchita izi ndi ulamuliro wotani? Ndipo ndani anakupatsani ulamuliro wotere?


Koma ansembe aakulu ndi akulu anapangira anthu kuti apemphe Barabasi, koma kuti aononge Yesu.


Koma ansembe aakulu anasonkhezera khamulo, kuti makamaka awamasulire Barabasi.


Mau awa analankhula m'nyumba yosungiramo chuma cha Mulungu pophunzitsa mu Kachisi; ndipo palibe munthu anamgwira Iye, pakuti nthawi yake siinafike.


Pamenepo anatola miyala kuti amponye Iye; koma Yesu anabisala, natuluka mu Kachisi.


Koma Ayuda anakakamiza akazi opembedza ndi omveka, ndi akulu a mzindawo, nawautsira chizunzo Paulo ndi Barnabasi, ndipo anawapirikitsa iwo m'malire ao.


Ndipo mzinda wonse unasokonezeka, ndipo anthu anathamangira pamodzi; nagwira Paulo namkoka kumtulutsa mu Kachisi; ndipo pomwepo pamakomo panatsekedwa.


Ndipo adamumva kufikira mau awa; ndipo anakweza mau ao nanena, Achoke padziko lapansi munthu wotere; pakuti sayenera iye kukhala ndi moyo.


Koma m'mene anagwira Petro ndi Yohane, anawathamangira pamodzi anthu onse kukhonde lotchedwa la Solomoni, alikudabwa ndithu.


Ndipo mwa manja a atumwi zizindikiro ndi zozizwa zambiri zinachitidwa pa anthu; ndipo anali onse ndi mtima umodzi m'khonde la Solomoni.


nanena, Tidakulamulirani chilamulire, musaphunzitsa kutchula dzina ili; ndipo taonani, mwadzaza Yerusalemu ndi chiphunzitso chanu, ndipo mufuna kutidzetsera ife mwazi wa munthu uja.


pakuti tinamumva iye alikunena, kuti, Yesu Mnazarayo amene adzaononga malo ano, nadzasanduliza miyambo imene Mose anatipatsa.


Ndipo msonkhano wonse wa ana a Israele unasonkhana ku Silo, nuutsa komweko chihema chokomanako; ndipo dziko linawagonjera.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa