Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 26:4 - Buku Lopatulika

4 Ndipo iwe uziti kwa iwo, Yehova atero: Ngati simudzandimvera Ine kuyenda m'chilamulo changa, chimene ndachiika pamaso panu,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo iwe uziti kwa iwo, Yehova atero: Ngati simudzandimvera Ine kuyenda m'chilamulo changa, chimene ndachiika pamaso panu,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Ukaŵauze kuti, Chauta akuti: Ngati simundimvera Ine, ngati simutsata malamulo amene ndidakupatsani,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Ukawawuze kuti, ‘Yehova akuti: Ngati simundimvera Ine ndi kuleka kutsatira malamulo anga, amene ndakupatsani,

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 26:4
22 Mawu Ofanana  

Koma mukadzabwerera pang'ono pokha osanditsata, kapena inu, kapena ana anu, osasunga malamulo anga ndi malemba anga amene ndawaika pamaso panu; mukadzatumikira milungu ina ndi kuilambira;


koma ngati mukana ndi kupanduka, mudzathedwa ndi lupanga; chifukwa m'kamwa mwa Yehova mwatero.


Koma ngati simudzamvera Ine kulipatula tsiku la Sabata, kusanyamula katundu ndi kulowa pa zipata za Yerusalemu tsiku la Sabata; pamenepo ndidzayatsa moto m'zipata zakezo, ndipo udzatha zinyumba za Yerusalemu, osazimidwanso.


Koma ngati simudzamva mau amenewa, Ine ndilumbira, pali Ine mwini, ati Yehova, nyumba iyi idzakhala yabwinja.


ndipo analowa, nakhalamo; koma sanamvere mau anu, sanayende m'chilamulo chanu; sanachite kanthu ka zonse zimene munawauza achite; chifukwa chake mwafikitsa pa iwo choipa chonsechi;


Sanadzichepetse mpaka lero lomwe, sanaope, sanayende m'chilamulo changa, kapena m'malemba anga, amene ndinaika pamaso panu ndi pa makolo anu.


Chifukwa mwafukiza, ndi chifukwa mwachimwira Yehova, osamvera mau a Yehova, osayenda m'chilamulo chake, ndi m'malemba ake, ndi m'mboni zake, chifukwa chake choipachi chakugwerani, monga lero lomwe.


chifukwa chake ndidzaichitira nyumba iyi, imene itchedwa dzina langa, imene mukhulupirirayi, ndipo ndidzachitira malo amene ndinakupatsani inu ndi makolo anu, monga ndinachitira Silo.


Potero samalirani kuchita malemba ndi maweruzo onse ndiwaika pamaso panu lero lino.


Pakuti nditakalowetsa awa m'dziko limene ndinalumbirira makolo ao, moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi; ndipo atadya nakhuta, nanenepa, pamenepo adzatembenukira milungu ina, ndi kuitumikira, ndi kundipeputsa Ine, ndi kuthyola chipangano changa.


Ndipo ichi ndi chilamulo Mose anachiika pamaso pa ana a Israele;


Ndipo mtundu waukulu wa anthu ndi uti, wakukhala nao malemba ndi maweruzo olungama, akunga chilamulo ichi chonse ndichiika pamaso panu lero lino?


kuti mwa zinthu ziwiri zosasinthika, m'mene Mulungu sangathe kunama, tikakhale nacho chotichenjeza cholimba, ife amene tidathawira kuchigwira chiyembekezo choikika pamaso pathu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa