Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 26:11 - Buku Lopatulika

11 Ndipo ansembe ndi aneneri ananena kwa akulu ndi kwa anthu onse, kuti, Munthu uyu ayenera kufa; pakuti wanenera mzinda uwu monga mwamva ndi makutu anu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Ndipo ansembe ndi aneneri ananena kwa akulu ndi kwa anthu onse, kuti, Munthu uyu ayenera kufa; pakuti wanenera mudzi uwu monga mwamva ndi makutu anu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Pamenepo ansembe ndi aneneri adauza akuluakuluwo ndi anthu ena onse kuti, “Munthu ameneyu ndi woyenera kumupha, chifukwa choti amalosa zoipa za mzinda uno, monga inu nomwe mwadzimvera.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Pamenepo ansembe ndi aneneri anawuza ndunazo pamodzi ndi anthu onse kuti, “Munthu uyu ayenera kuphedwa chifukwa amalosera zoyipira mzinda uno. Inu mwadzimvera nokha zimenezi!”

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 26:11
13 Mawu Ofanana  

Koma, Yehova, mudziwa uphungu wao wonse wakundinenera ine kundipha ine; musakhulukire mphulupulu yao, musafafanize tchimo lao pamaso panu; aphunthwitsidwe pamaso panu; muchite nao m'nthawi ya mkwiyo wanu.


Pamenepo akulu ndi anthu onse anati kwa ansembe ndi kwa aneneri, Munthu uyu sayenera kufa: pakuti watinenera ife m'dzina la Yehova Mulungu wathu.


Ndipo akulu anati kwa mfumu, Munthu uyu aphedwetu; chifukwa analopetsa manja a anthu a nkhondo otsala m'mzinda muno, ndi manja a anthu onse, pakunena kwa iwo mau otero; pakuti munthu uyu safuna mtendere wa anthu awa, koma nsautso yao.


muganiza bwanji? Iwo anayankha nati, Ali woyenera kumupha.


Anayankha nati kwa iye, Akadakhala wosachita zoipa uyu sitikadampereka Iye kwa inu.


Ayuda anamyankha iye, Tili nacho chilamulo ife, ndipo monga mwa chilamulocho ayenera kufa, chifukwa anadziyesera Mwana wa Mulungu.


Ndipo adamumva kufikira mau awa; ndipo anakweza mau ao nanena, Achoke padziko lapansi munthu wotere; pakuti sayenera iye kukhala ndi moyo.


Koma mneneri wakuchita modzikuza ndi kunena mau m'dzina langa, amene sindinamlamulire anene, kapena kunena m'dzina la milungu ina, mneneri ameneyo afe.


Pamenepo amuna akumudziwo anati kwa Yowasi, Umtulutse mwana wako kuti afe; pakuti anagamula guwa la nsembe la Baala, pakutinso analikha chifanizo chinali pomwepo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa