Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 24:9 - Buku Lopatulika

9 Ndipo ndidzawapatsa akhale choopsetsa choipa ku maufumu a dziko lapansi; akhale chitonzo ndi nkhani ndi choseketsa, ndi chitemberero, monse m'mene ndidzawapirikitsiramo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo ndidzawapatsa akhale choopsetsa choipa ku maufumu a dziko lapansi; akhale chitonzo ndi nkhani ndi choseketsa, ndi chitemberero, monse m'mene ndidzawapirikitsiramo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Ndidzaŵasandutsa chinthu chonyansa kwa anthu a maufumu onse a pa dziko lapansi, chinthu chonyozeka, chinthu chopanda pake, chinthu chomachiseka ndi chotembereredwa kulikonse kumene ndidzaŵapirikitsire.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Ndidzawasandutsa chinthu chonyansa kwa maufumu onse a dziko lapansi, chinthu chonyozeka ndi chopandapake, chinthu chochitidwa chipongwe ndi chotembereredwa kulikonse kumene ndidzawabalalitsira.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 24:9
29 Mawu Ofanana  

pamenepo Ine ndidzalikha Aisraele kuwachotsera m'dziko ndidawapatsali; ndipo nyumba ino ndapatulira dzina langayi ndidzaitaya kosapenyeka; ndipo Israele adzakhala ngati mwambi ndi nkhani pakati pa anthu onse.


pamenepo ndidzawazula m'dziko langa limene ndinawapatsa; ndi nyumba ino ndinaipatulira dzina langa ndidzaitaya, osaionanso, ndi kuiyesa mwambi ndi mnyozo mwa mitundu yonse ya anthu.


Ndipo chovala changa ndinayesa chiguduli, koma amandiphera mwambi.


Chifukwa chake ndidzaipitsa akulu a Kachisi, ndipo ndidzasanduliza Yakobo akhale temberero, ndi Israele akhale chitonzo.


Ndipo mudzasiya dzina lanu likhale chitemberero kwa osankhidwa anga, ndipo Ambuye Yehova adzakupha iwe, nadzatcha atumiki ake dzina lina;


Ndipo ndidzawapereka akhale oopsetsa m'maufumu onse a dziko lapansi, chifukwa cha Manase mwana wa Hezekiya mfumu ya Yuda, chifukwa cha zija anachita mu Yerusalemu.


Ndipo ndidzayesa mzindawu chodabwitsa, ndi chotsonyetsa; onse amene adzapitapo adzadabwa ndi kutsonya chifukwa cha zopanda pake zonse.


Yerusalemu, ndi mizinda ya Yuda, ndi mafumu ake omwe, ndi akulu ake, kuwayesa iwo bwinja, chizizwitso, chotsonyetsa, ndi chitemberero; monga lero lino;


pamenepo ndidzayesa nyumba iyi ifanane ndi Silo, ndipo ndidzayesa mzinda uwu chitemberero cha kwa mitundu yonse ya dziko lapansi.


Ndipo ndidzatsata iwe ndi lupanga, ndi njala, ndi mliri, ndipo ndidzawapereka akhale oopsetsa m'maufumu onse a dziko lapansi, akhale chitemberero, ndi chodabwitsa, ndi chotsonyetsa, ndi chitonzo, kwa mitundu yonse kumene ndinawapirikitsirako;


ndipo am'nsinga onse a Yuda amene ali mu Babiloni adzatemberera pali iwo, kuti, Yehova akuchitire iwe monga Zedekiya ndi Ahabu, amene mfumu ya ku Babiloni inaotcha m'moto;


Chifukwa chake Yehova atero: Simunandimvere Ine, kuti mulalikire ufulu, munthu yense kwa mbale wake, ndi munthu yense kwa mnzake; taonani, ndilalikira kwa inu ufulu, ati Yehova, wa kulupanga, kumliri, ndi kunjala; ndipo ndidzakuperekani mukhale oopsetsa m'maufumu onse a dziko lapansi.


Pakuti atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Monga mkwiyo wanga ndi ukali wanga wathiridwa kwa okhala mu Yerusalemu, momwemo ukali wanga udzathiridwa pa inu, pamene mudzalowa mu Ejipito; ndipo mudzakhala chitukwano, ndi chizizwitso, ndi chitemberero, ndi chitonzo; ndipo simudzaonananso malo ano.


Ndipo ndidzatenga otsala a Yuda, amene analozetsa nkhope zao alowe m'dziko la Ejipito akhale m'menemo, ndipo adzathedwa onse; m'dziko la Ejipito adzagwa, adzathedwa ndi lupanga ndi njala; adzafa kuyambira wamng'ono mpaka wamkulu, ndi lupanga ndi njala; ndipo adzakhala chitukwano, ndi chizizwitso, ndi chitemberero, ndi chitonzo.


Ndipo ndidzalanga iwo okhala m'dziko la Ejipito, monga ndinalanga Yerusalemu, ndi lupanga, ndi njala, ndi mliri;


Ndipo Yehova sanathe kupirirabe, chifukwa cha machitidwe anu oipa, ndi chifukwa cha zonyansa zimene munazichita; chifukwa chake dziko lanu likhala bwinja, ndi chizizwitso, ndi chitemberero, lopanda wokhalamo, monga lero lomwe.


Pakuti atero Ambuye Yehova, Ndidzawakweretsera msonkhano wa anthu, ndi kuwapereka awazunze, ndi kulanda chuma chao.


nunene kwa ana a Amoni, Tamverani mau a Ambuye Yehova, Atero Ambuye Yehova, Popeza unati, Ha! Kunena malo anga opatulika; muja anadetsedwa ndi kunena dziko la Israele; muja linapasuka ndi kunena nyumba ya Yuda; muja adalowa kundende;


Wobadwa ndi munthu iwe, popeza Tiro ananyodola Yerusalemu, ndi kuti, Ha! Wathyoka uwu udali chipata cha mitundu ya anthu; wanditembenukira ine; ndidzakhuta ine, wapasuka uwu;


chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Taona ndidzatsutsana nawe Inedi, ndi kuchita maweruzo pakati pako pamaso pa amitundu.


Yehova adzalola adani anu akukantheni; mudzawatulukira njira imodzi, koma mudzawathawa pamaso pao njira zisanu ndi ziwiri, ndipo mudzagwedezeka pakati pa maufumu onse a dziko lapansi.


Ndipo mudzakhala chodabwitsa, ndi nkhani, ndi mwambi, mwa mitundu yonse ya anthu amene Yehova akutsogoleraniko.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa