Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 24:10 - Buku Lopatulika

10 Ndipo ndidzatuma lupanga, ndi njala, ndi mliri mwa iwo, mpaka athedwa m'dziko limene ndinapatsa iwo ndi makolo ao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Ndipo ndidzatuma lupanga, ndi njala, ndi chaola mwa iwo, mpaka athedwa m'dziko limene ndinapatsa iwo ndi makolo ao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Ndidzaŵapha ndi nkhondo, njala ndi mliri, mpaka onsewo nditaŵapululiratu m'dziko limene ndidaŵapatsa iwowo ndi makolo ao.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Ndidzawatumizira nkhondo, njala ndi mliri mpaka atawonongedwa mʼdziko limene ndinawapatsa iwo ndi makolo awo.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 24:10
27 Mawu Ofanana  

Popeza Yehova adzawakantha Aisraele monga bango ligwedezeka ndi madzi, nadzazula Aisraele m'dziko lino labwino analipatsa makolo ao, nadzawamwazira ku tsidya lija la Yufurate, popeza iwo anapanga zifanizo zao zokwiyitsa Yehova.


Izi ziwiri zakugwera; ndani adzakulira iwe? Bwinja ndi chipasuko, njala ndi lupanga; ndidzatonthoza mtima wako bwanji?


Pamene asala chakudya, sindidzamva kufuula kwao; ndipo pamene apereka nsembe yopsereza, ndi nsembe yaufa sindidzawalandira; koma ndidzawatha ndi lupanga, ndi chilala, ndi mliri.


Ndipo padzakhala, pamene adzati kwa iwe, Titulukire kuti? Pamenepo uziti, Atero Yehova: Amene a kuimfa, anke kuimfa; amene a kulupanga, anke kulupanga; amene a kunjala, anke kunjala; ndi amene a kunsinga, anke kunsinga.


Adzafa ndi imfa zanthenda; sadzaliridwa maliro, sadzaikidwa; adzakhala ngati ndowe panthaka; ndipo adzathedwa lupanga, ndi njala; ndipo mitembo yao idzakhala chakudya cha mbalame za kumlengalenga, ndi zilombo za dziko lapansi.


Ndipo ndidzataya uphungu wa Yuda ndi wa Yerusalemu m'malo ano; ndipo ndidzagwetsa iwo ndi lupanga pamaso pa adani ao, ndi padzanja la iwo amene afuna moyo wao; mitembo yao ndidzapatsa ikhale chakudya cha mbalame za m'mlengalenga, ndi cha zilombo za dziko lapansi.


Iye amene akhala m'mzinda uwu adzafa ndi lupanga, ndi njala, ndi mliri; koma iye amene atuluka, napandukira kwa Ababiloni akuzinga inu, adzakhala ndi moyo, ndipo moyo wake udzapatsidwa kwa iye ngati chofunkha.


Ndipo padzakhala, kuti mtundu ndi ufumu umene sudzamtumikira Nebukadinezara yemweyo mfumu ya ku Babiloni, mtundu umenewo Ine ndidzalanga, ati Yehova, ndi lupanga, ndi njala, ndi mliri, mpaka nditatha onse ndi dzanja lake.


Yehova wa makamu atero: Taonani, ndidzatuma pa iwo lupanga, ndi njala, ndi mliri, ndipo ndidzayesa iwo onga nkhuyu zoola, zosadyeka, pokhala nzoipa.


Ndipo ndidzatsata iwe ndi lupanga, ndi njala, ndi mliri, ndipo ndidzawapereka akhale oopsetsa m'maufumu onse a dziko lapansi, akhale chitemberero, ndi chodabwitsa, ndi chotsonyetsa, ndi chitonzo, kwa mitundu yonse kumene ndinawapirikitsirako;


taonani mitumbira, yafika kumzinda kuugwira, ndipo mzinda uperekedwa m'dzanja la Ababiloni olimbana nao, chifukwa cha lupanga, ndi chifukwa cha njala, ndi chifukwa cha mliri; ndipo chimene munachinena chaoneka; ndipo, taonani, muchiona.


Ndipo Inu Yehova Mulungu mwati kwa ine, Udzigulire munda ndi ndalama, nuitane mboni; koma mzinda waperekedwa m'manja a Ababiloni.


Chifukwa chake Yehova atero: Simunandimvere Ine, kuti mulalikire ufulu, munthu yense kwa mbale wake, ndi munthu yense kwa mnzake; taonani, ndilalikira kwa inu ufulu, ati Yehova, wa kulupanga, kumliri, ndi kunjala; ndipo ndidzakuperekani mukhale oopsetsa m'maufumu onse a dziko lapansi.


Kudzatero ndi anthu onse akulozetsa nkhope zao anke ku Ejipito kuti akhale kumeneko; adzafa ndi lupanga, ndi njala, ndi mliri; ndipo wa iwo sadzatsala kapena kupulumuka ku choipa chimene ndidzatengera pa iwo ngakhale mmodzi yense.


Tsopano mudziwetu kuti mudzafa ndi lupanga, ndi njala ndi mliri, komwe mufuna kukakhalako.


Akana Yehova, ndi kuti, Si ndiye; choipa sichidzatifika ife; sitidzaona kapena lupanga kapena njala;


chifukwa chake atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, Taonani, ndidzadyetsa anthu awa chivumulo, ndi kuwamwetsa madzi andulu.


Ndidzawabalalitsanso mwa amitundu, amene iwo kapena makolo ao sanawadziwe; ndipo ndidzatumiza lupanga, liwatsate mpaka ndawatha.


Uzitero nao, Atero Ambuye Yehova, Pali Ine, iwo okhala kumabwinja adzagwadi ndi lupanga, ndi iye ali kuthengo koyera ndidzampereka kwa zilombo, adyedwe nazo; ndi iwo okhala m'malinga ndi m'mapanga adzafa ndi mliri.


Atero Yehova Mulungu, Omba manja ako, ponda ndi phazi lako, nuti, Kalanga ine, chifukwa cha zonyansa zoipa zonse za nyumba ya Israele; pakuti adzagwa ndi lupanga, ndi njala, ndi mliri.


Kunja kuli lupanga, ndi m'katimo muli mliri ndi njala; wokhala kuthengo adzafa ndi lupanga, ndi wokhala m'mzindawo njala ndi mliri zidzamutha.


Yehova adzakumamatiritsani mliri, kufikira akakuthani kukuchotsani kudziko, kumene mupitako kulilandira.


Ndipo ndinapenya, taonani, kavalo wotumbuluka; ndipo iye womkwera, dzina lake ndiye Imfa; ndipo dziko la akufa linatsatana naye; ndipo anawapatsa ulamuliro pa dera lachinai la dziko, kukapha ndi lupanga, ndi njala, ndi imfa, ndi zilombo za padziko.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa