Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 24:2 - Buku Lopatulika

2 Dengu limodzi linali ndi nkhuyu zabwinobwino, ngati nkhuyu zoyamba kucha; ndipo dengu limodzi linali ndi nkhuyu zoipaipa, zosadyeka, zinali zoipa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Dengu limodzi linali ndi nkhuyu zabwinobwino, ngati nkhuyu zoyamba kucha; ndipo dengu limodzi linali ndi nkhuyu zoipaipa, zosadyeka, zinali zoipa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 M'dengu lina munali nkhuyu zabwino kwambiri, ngati nkhuyu zoyambirira kupsa. Koma m'dengu linalo munali nkhuyu zoipa kwambiri, zosatinso nkudyeka.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Mʼdengu limodzi munali nkhuyu zabwino kwambiri, ngati nkhuyu zoyambirira kucha. Mʼdengu linalo munali nkhuyu zoyipa kwambiri zosati nʼkudya.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 24:2
11 Mawu Ofanana  

Ndikanachitanso chiyani ndi munda wanga wampesa, chimene sindinachite m'menemo; muja ndinayembekeza kuti udzabala mphesa, wabaliranji mphesa zosadya?


Chifukwa kuti munda wampesa wa Yehova wa makamu ndiwo banja la Israele, ndi anthu a Yuda, mtengo wake womkondweretsa; Iye nayembekeza chiweruziro, koma onani kuphana; nayembekeza chilungamo, koma onani kufuula.


Yehova wa makamu atero: Taonani, ndidzatuma pa iwo lupanga, ndi njala, ndi mliri, ndipo ndidzayesa iwo onga nkhuyu zoola, zosadyeka, pokhala nzoipa.


Ndinapeza Israele ngati mphesa m'chipululu, ndinaona makolo anu ngati chipatso choyamba cha mkuyu nyengo yake yoyamba; koma anadza kwa Baala-Peori, nadzipatulira chonyansacho, nasandulika onyansa, chonga chija anachikonda.


Kalanga ine! Pakuti ndikunga atapulula zipatso za m'mwamvu, atakunkha m'munda wampesa; palibe mphesa zakudya; moyo wanga ukhumba nkhuyu yoyamba kupsa.


Malinga ako onse adzanga mikuyu ndi nkhuyu zoyamba kupsa; akagwedeza zingokugwa m'kamwa mwa wakudya.


Zipatso zoyamba zonse zili m'dziko mwao, zimene amadza nazo kwa Yehova, zikhale zako; oyera onse a m'banja lako adyeko.


Inu ndinu mchere wa dziko lapansi; koma mcherewo ngati ukasukuluka, adzaukoleretsa ndi chiyani? Pamenepo sungakwanirenso kanthu konse, koma kuti ukaponyedwe kunja, nupondedwe ndi anthu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa