Yeremiya 24:1 - Buku Lopatulika1 Yehova anandionetsa ine, ndipo, taonani, madengu awiri a nkhuyu oikidwa pakhomo pa Kachisi wa Yehova; Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni atachotsa am'nsinga Yekoniya mwana wake wa Yehoyakimu, mfumu ya Yuda, ndi akulu a Yuda, ndi amisiri ndi achipala, kuwachotsa ku Yerusalemu, nawatengera ku Babiloni. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20141 Yehova anandionetsa ine, ndipo, taonani, madengu awiri a nkhuyu oikidwa pakhomo pa Kachisi wa Yehova; Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni atachotsa am'nsinga Yekoniya mwana wake wa Yehoyakimu, mfumu ya Yuda, ndi akulu a Yuda, ndi amisiri ndi achipala, kuwachotsa ku Yerusalemu, nawatengera ku Babiloni. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa1 Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni, adaatenga ukapolo Yehoyakini, mwana wa Yehoyakimu mfumu ya ku Yuda, kuchoka naye ku Yerusalemu. Adaatenganso ukapolo akalonga onse a ku Yuda, anthu aluso ndi akatswiri enanso kupita nawo ku Babiloni. Nthaŵi imeneyo Chauta adandiwonetsa zinthu zina m'masomphenya, zinthuzo ndi izi: ndidaona madengu aŵiri a nkhuyu ali pakhomo pa Nyumba ya Chauta. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero1 Nebukadinezara, mfumu ya ku Babuloni anatenga ukapolo Yekoniya mwana wa Yehoyakimu mfumu ya ku Yuda pamodzi ndi nduna zake, anthu aluso ndi akatswiri a ku Yuda ndi kupita nawo ku Babuloni. Pambuyo pake Yehova anandionetsa madengu awiri a nkhuyu atayikidwa pa khomo pa Nyumba ya Yehova. Onani mutuwo |