Yeremiya 21:4 - Buku Lopatulika4 Yehova, Mulungu wa Israele atero, Taonani, ndidzabweza zida za nkhondo zimene zili m'manja anu, zimene mumenyana nazo ndi mfumu ya ku Babiloni, ndi Ababiloni akuzinga inu, kunja kwa malinga, ndipo ndidzazisonkhanitsa pakati pa mzinda uwu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20144 Yehova, Mulungu wa Israele atero, Taonani, ndidzabweza zida za nkhondo zimene zili m'manja anu, zimene mumenyana nazo ndi mfumu ya ku Babiloni, ndi Ababiloni akuzinga inu, kunja kwa malinga, ndipo ndidzazisonkhanitsa pakati pa mudzi uwu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa4 “Mukamuuze Zedekiya kuti Chauta, Mulungu wa Israele akuti, ‘Ndidzakulandani zida zankhondo zimene zili m'manja mwanuzo, zimene mukumenya nazo nkhondo ndi mfumu ya ku Babiloni ndi ankhondo ake amene akuzingani ndi zithando zankhondo. Ndidzabwera nazo ndi kuziika m'kati mwa mzinda uno. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero4 ‘Yehova, Mulungu wa Israeli akuti ndikulandeni zida zimene zili mʼmanja mwanu zimene mukugwiritsa ntchito polimbana ndi mfumu ya ku Babuloni ndi ankhondo ake amene akuzingani kunja kwa lingali. Ndipo ndidzasonkhanitsa zidazo mʼkati mwa mzindawu. Onani mutuwo |
Pakuti Yehova atero, Taonani, ndidzakuyesa iwe choopsa cha kwa iwe mwini, ndi kwa abwenzi ako onse; ndipo iwo adzagwa ndi lupanga la adani ao, ndipo maso ako adzaona; ndipo ndidzapereka Ayuda onse m'dzanja la mfumu ya ku Babiloni, ndipo iye adzawatengera iwo am'nsinga ku Babiloni, nadzawapha ndi lupanga.