Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 21:5 - Buku Lopatulika

5 Ndipo Ine mwini ndidzamenyana ndi inu ndi dzanja lotambasuka ndi mkono wamphamvu, m'mkwiyo, ndi m'kupsa mtima, ndi mu ukali waukulu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Ndipo Ine mwini ndidzamenyana ndi inu ndi dzanja lotambasuka ndi mkono wamphamvu, m'mkwiyo, ndi m'kupsa mtima, ndi m'ukali waukulu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Ineyo mwiniwakene ndi mkono wanga wamphamvu, ndidzamenyana nanu nkhondo inuyo, ndili wopsa mtima, wokalipa ndi wokwiya.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Ineyo mwini wakene ndi mkono wotambasula ndi dzanja lamphamvu, ndidzachita nanu nkhondo ndili wokwiya, wokalipa ndi waukali.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 21:5
21 Mawu Ofanana  

Chifukwa chake nena kwa ana a Israele Ine ndine Yehova, ndipo ndidzakutulutsani pansi pa akatundu a Aejipito ndipo ndidzakulanditsani ku ukapolo wanu; ndipo ndidzakuombolani ndi dzanja lotambasuka, ndi maweruzo aakulu;


Pakuti ndatambasula dzanja langa tsopano, kuti ndikupande iwe ndi anthu ako ndi mliri, ndi kuti uonongeke padziko lapansi.


Adzangoweramira pansi pa andende, ndipo adzagwa pansi pa ophedwa. Mwa izi zonse mkwiyo wake sunachoke, koma dzanja lake lili chitambasulire.


Chifukwa chake mkwiyo wa Yehova wayaka pa anthu ake, ndipo Iye watambasulira iwo dzanja lake, nawakantha, ndipo zitunda zinanthunthumira, ndi mitembo yao inali ngati zinyatsi pakati pa makwalala. Mwa izi zonse mkwiyo wake sunachoke, koma dzanja lake lili chitambasulire.


Koma iwo anapandukira ndi kumvetsa chisoni mzimu wake woyera, chifukwa chake Iye anasandulika mdani wao, nawathira nkhondo Iye yekha.


Aramu patsogolo ndi Afilisti pambuyo; ndipo iwo adzadya Israele ndi kukamwa koyasama. Mwa izi zonse mkwiyo wake sunachoke, koma dzanja lake lili chitambasulire.


Chifukwa chake Ambuye sadzakondwera ndi anyamata ao, ngakhale kuwachitira chifundo amasiye ao ana ndi akazi; popeza yense ali wodetsa ndi wochimwa, m'kamwa monse mulankhula zopusa. Mwa izi zonse mkwiyo wake sunachoke, koma dzanja lake lili chitambasulire.


Manase adzadya Efuremu; ndi Efuremu adzadya Manase, ndipo iwo pamodzi adzadyana ndi Yuda. Mwa izi zonse mkwiyo wake sunachoke, koma dzanja lake lili chitambasulire.


Ha! Yehova Mulungu, taonani, Inu munalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi mphamvu yanu yaikulu ndi mkono wanu wotambasuka; palibe chokanika Inu;


Taonani, ndidzawasokolotsa m'maiko monse, kumene ndinawapirikitsira ndi mkwiyo wanga, ndi m'kupsa mtima kwanga, ndi mu ukali waukulu, ndipo ndidzawabwezeranso kumalo kuno, ndipo ndidzawakhazikitsa mokhulupirika,


Kapena pembedzero lao lidzagwa pamaso pa Yehova, ndipo adzabwerera yense kuleka njira yake yoipa; pakuti mkwiyo ndi ukali umene Yehova wanenera anthu awa ndi waukulu.


Pakuti ngakhale mukadakantha nkhondo yonse ya Ababiloni akumenyana nanu, ngakhale akadatsala olasidwa okhaokha mwa iwo, koma iwowa akadauka yense m'hema wake ndi kutentha mzinda uwu ndi moto.


Nyumba zao zidzasanduka za ena, pamodzi ndi minda yao ndi akazi ao; pakuti ndidzatambasula dzanja langa pa okhala m'dziko, ati Yehova.


Pokwiya moopsa walikha nyanga zonse za Israele; wabweza m'mbuyo dzanja lake lamanja pamaso pa adaniwo, natentha Yakobo ngati moto wamalawi wonyambita mozungulira.


ndipo ndidzakantha uta wako kuuchotsa m'dzanja lako lamanzere, ndi kutayitsa mivi yako kudzanja lako lamanja.


chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Taona ndidzatsutsana nawe Inedi, ndi kuchita maweruzo pakati pako pamaso pa amitundu.


Dzichenjerani, mungaiwale chipangano cha Yehova Mulungu wanu, chimene anapangana nanu, ndi kuti mungadzipangire fano losema, chifaniziro cha kanthu kalikonse Yehova Mulungu wanu anakuletsani.


Kapena kodi anayesa Mulungu kumuka ndi kudzitengera mtundu mwa mtundu wina wa anthu, ndi mayesero, ndi zizindikiro, ndi zozizwa, ndi nkhondo, ndi mwa dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, ndi mwa zoopsa zazikulu, monga mwa zonse Yehova Mulungu wanu anakuchitirani mu Ejipito pamaso panu?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa