Yeremiya 21:2 - Buku Lopatulika2 Tifunsirenitu ife kwa Yehova; pakuti Nebukadinezara mfumu wa ku Babiloni atithira ife nkhondo; kapena Yehova adzatichitira ife monga mwa ntchito zake zolapitsa, kuti atichokere. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20142 Tifunsirenitu ife kwa Yehova; pakuti Nebukadinezara mfumu wa ku Babiloni atithira ife nkhondo; kapena Yehova adzatichitira ife monga mwa ntchito zake zolapitsa, kuti atichokere. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa2 “Pitani kwa Yeremiya mukampemphe kuti atinenere kwa Chauta, popeza kuti Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni akufuna kutithira nkhondo. Mwina mwake Chauta nkutichitira zodabwitsa, kuti Nebukadinezara achoke kwathu kuno.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero2 Iwo amati akanene kwa Yeremiya mawu akuti, “Tinenere kwa Yehova chifukwa Nebukadinezara mfumu ya Babuloni akutithira nkhondo. Mwina mwake Yehova nʼkutichitira zodabwitsa kuti Nebukadinezarayo achoke kwathu kuno.” Onani mutuwo |
Ndipo Samuele ananena ndi Saulo, Wandivutiranji kundikweretsa kuno? Saulo nayankha, Ndilikusautsika kwambiri, pakuti Afilisti aponyana nkhondo ndi ine, ndipo Mulungu anandichokera, osandiyankhanso, kapena ndi aneneri, kapena ndi maloto; chifukwa chake ndakuitanani, kuti mundidziwitse chimene ndiyenera kuchita.