Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 21:1 - Buku Lopatulika

1 Mau amene anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova, pamene Zedekiya mfumu anatuma kwa iye Pasuri mwana wa Malikiya, ndi Zefaniya mwana wake wa Maaseiya wansembe, akati,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Mau amene anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova, pamene Zedekiya mfumu anatuma kwa iye Pasuri mwana wa Malikiya, ndi Zefaniya mwana wake wa Maaseiya wansembe, akati,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Zedekiya, mfumu ya ku Yuda, adatuma Pasuri mwana wa Malakiya, ndiponso wansembe Zefaniya mwana wa Maseiya, naŵauza kuti,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Mfumu Zedekiya inatuma Pasuri mwana wa Malikiya ndi wansembe Zefaniya mwana wa Maseya kwa Yeremiya.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 21:1
20 Mawu Ofanana  

Mukani, funsirani ine, ndi anthu, ndi Yuda yense, kwa Yehova za mau a buku ili adalipeza; pakuti mkwiyo wa Yehova wotiyakira ife ndi waukulu; popeza atate athu sanamvere mau a buku ili, kuchita monga mwa zonse zotilemberamo.


Ndi ana a Yosiya: woyamba Yohanani, wachiwiri Yehoyakimu, wachitatu Zedekiya, wachinai Salumu.


ndi Adaya mwana wa Yerohamu, mwana wa Pasuri, mwana wa Malikiya, ndi Maasai mwana wa Adiyele, mwana wa Yazera, mwana wa Mesulamu, mwana wa Mesilemiti, mwana wa Imeri,


Pakuti Iye anawakweretsera mfumu ya Ababiloni, ndiye anawaphera anyamata ao ndi lupanga, m'nyumba ya malo ao opatulika, osachitira chifundo mnyamata kapena namwali, mkulu kapena nkhalamba; Mulungu anawapereka onse m'dzanja lake.


ndi abale ao ochita ntchito ya m'nyumbayi ndiwo mazana asanu ndi atatu mphambu makumi awiri kudza awiri; ndi Adaya mwana wa Yerohamu, mwana wa Pelaliya, mwana wa Amizi, mwana wa Zekariya, mwana wa Pasuri, mwana wa Malikiya;


Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, kuti, Chifukwa watumiza makalata m'dzina lako iwe mwini kwa anthu onse amene akhala ku Yerusalemu, ndi kwa Zefaniya mwana wake wa Maaseiya wansembe, ndi kwa ansembe onse, kuti,


Ndipo Zefaniya wansembe anawerenga kalata amene m'makutu a Yeremiya mneneri.


ndipo ndinawalowetsa m'nyumba ya Yehova, m'chipinda cha ana a Hanani mwana wa Igadaliya, munthu wa Mulungu, chokhala pambali pa chipinda cha akulu, ndicho chosanjika pa chipinda cha Maaseiya mwana wa Salumu, mdindo wa pakhomo;


Ndipo Zedekiya mwana wa Yosiya anakhala mfumu m'malo a Koniya mwana wa Yehoyakimu, amene Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni inamlowetsa mfumu m'dziko la Yuda.


pamenepo Zedekiya mfumu inatuma, ndi kumtenga iye; ndipo mfumu inamfunsa iye m'tseri m'nyumba mwake, niti, Kodi alipo mau ochokera kwa Yehova? Ndipo Yeremiya, anati, Alipo. Anatinso, Mudzaperekedwa m'dzanja la mfumu ya ku Babiloni.


Ndipo Zedekiya mfumu anatuma Yehukala mwana wa Selemiya, ndi Zefaniya mwana wa Maaseiya wansembe, kwa Yeremiya mneneri, kukanena, Mutipemphereretu kwa Yehova Mulungu wathu.


Atero Yehova, Mulungu wa Israele: Muzitero kwa mfumu ya Yuda, imene inakutumani inu kwa Ine kuti mundifunse Ine: Taonani, nkhondo ya Farao, yakutulukira kudzathandiza inu, idzabwerera ku Ejipito ku dziko lao.


Ndipo Sefatiya mwana wa Matani ndi Gedaliya mwana wa Pusuri, ndi Yukala mwana wa Selemiya, ndi Pasuri mwana wa Malikiya, anamva mau amene Yeremiya ananena ndi anthu onse, kuti,


Ndipo mfumu Zedekiya anatuma, namtenga Yeremiya mneneri nalowa naye m'khomo lachitatu la nyumba ya Yehova; ndipo mfumu inati kwa Yeremiya, Ndidzakufunsa iwe kanthu; usandibisire ine kanthu.


Ndipo kapitao wa alonda anatenga Seraya wansembe wamkulu, ndi Zefaniya wansembe wachiwiri, ndi akudikira pakhomo atatu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa