Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 12:2 - Buku Lopatulika

2 Inu Mwabzala iwo, inde, anagwiritsatu mizu; amera, inde, abalatu zipatso; muli pafupi m'kamwa mwao, muli patali ndi impso zao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Inu Mwabzala iwo, inde, anagwiritsatu mizu; amera, inde, abalatu zipatso; muli pafupi m'kamwa mwao, muli patali ndi impso zao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Inu mudaŵabzala, ndipo adamera mizu. Amakula, namabala zipatso. Amakonda kulankhula za Inu, koma mitima yao ili kutali ndi Inu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Inu munawadzala ndipo anamera mizu; amakula ndi kubereka zipatso. Dzina lanu limakhala pakamwa pawo nthawi zonse, koma mitima yawo imakhala kutali ndi Inu.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 12:2
15 Mawu Ofanana  

M'mzinda waukulu anthu abuula alinkufa; ndi moyo wa iwo olasidwa ufuula; koma Mulungu sasamalira choipacho.


Ndinapenya wopusa woyala mizu; koma pomwepo ndinatemberera pokhala pake.


Ndapenya woipa, alikuopsa, natasa monga mtengo wauwisi wanzika.


Ndipo Ambuye anati, Popeza anthu awa ayandikira ndi Ine ndi m'kamwa mwao, nandilemekeza ndi milomo yao, koma mtima wao uli kutali ndi Ine, ndi mantha ao akundiopa Ine, ndi lamulo la anthu analiphunzira;


Pakuti Yehova wa makamu, amene anakuoka iwe, wakunenera iwe choipa, chifukwa cha zoipa za nyumba ya Israele ndi nyumba ya Yuda, zimene anadzichitira okha pakuutsa mkwiyo wanga m'mene anafukizira Baala.


Ndipo zingakhale zonsezi Yuda mphwake wonyenga sanabwere kwa Ine ndi mtima wake wonse, koma monama, ati Yehova.


Uzitero naye, Yehova atero: Taonani, chimene ndamanga ndidzapasula, ndi chimene ndaoka ndidzazula; ndidzatero m'dziko lonseli.


Ndipo akudzera monga amadzera anthu, nakhala pansi pamaso pako ngati anthu anga, namva mau ako, koma osawachita; pakuti pakamwa pao anena mwachikondi, koma mtima wao utsata phindu lao.


Ndipo sanafuulire kwa Ine ndi mtima wao, koma alira pakama pao, asonkhanira tirigu ndi vinyo, apikisana ndi Ine.


Inu wa maso osalakwa, osapenya choipa, osakhoza kupenyerera chovuta, mupenyereranji iwo akuchita mochenjerera, ndi kukhala chete pamene woipa ammeza munthu wolungama woposa iye mwini;


Anthu awa andilemekeza Ine ndi milomo yao; koma mtima wao uli kutali ndi Ine.


Ndipo Iye ananena nao, Yesaya ananenera bwino za inu onyenga, monga mwalembedwa, Anthu awa andilemekeza Ine ndi milomo yao, koma mtima wao ukhala kutali ndi Ine.


Avomereza kuti adziwa Mulungu, koma ndi ntchito zao amkana Iye, popeza ali onyansitsa, ndi osamvera, ndi pa ntchito zonse zabwino osatsimikizidwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa