Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 11:8 - Buku Lopatulika

8 Koma sanamvere, sanatchere khutu lao, koma onse anayenda m'kuumirira kwa mtima wao woipa; chifukwa chake ndinatengera iwo mau onse a pangano ili, limene ndinauza iwo kuti achite, koma sanachite.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Koma sanamvere, sanatchere khutu lao, koma onse anayenda m'kuumirira kwa mtima wao woipa; chifukwa chake ndinatengera iwo mau onse a pangano ili, limene ndinauza iwo kuti achite, koma sanachite.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Koma sadamvere, sadalabadeko. Aliyense adangoti nkhongo gwa, kutsata makhalidwe a mtima wake woipa. Ndidaŵalamula kuti asunge chipangano changa, koma iwo sadachisunge. Nchifukwa chake ndidaŵalanga monga m'mene ndidaanenera.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Koma sanamvere kapena kulabadirako. Aliyense anawumirira kuchita zoyipa za mʼmitima yawo. Ngakhale ndinawalamulira kuti asunge pangano langa koma iwo sanasunge. Choncho ndinawalanga monga ndinaneneramo.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 11:8
31 Mawu Ofanana  

Koma anakhala osamvera, napandukira Inu, nataya chilamulo chanu m'mbuyo mwao napha aneneri anu akuwachitira umboni, kuwabwezera kwa Inu, nachita zopeputsa zazikulu.


ndipo munawachitira umboni, kuti muwabwezerenso ku chilamulo chanu; koma anachita modzikuza, osamvera malamulo anu; koma anachimwira malamulo anu (amene munthu akawachita adzakhala nao ndi moyo); nakaniza phewa lao, naumitsa khosi lao, osamvera.


Anthu oipa awa, amene akana kumva mau anga, amene ayenda m'kuumirira kwa mtima wao, atsata milungu ina kuitumikira, ndi kuigwadira, adzakhala ngati mpango uwu, wosayenera kanthu.


Pa nthawi yomweyo adzatcha Yerusalemu mpando wa Yehova; ndipo mitundu yonse idzasonkhanidwa kumeneko, ku dzina la Yehova, ku Yerusalemu; ndipo sadzayendanso konse m'kuumirira kwa mtima wao woipa.


si monga pangano limene ndinapangana ndi makolo ao tsiku lija ndinawagwira manja kuwatulutsa m'dziko la Ejipito; pangano langa limenelo analiswa, ngakhale ndinali mbuyao, ati Yehova.


ndipo analowa, nakhalamo; koma sanamvere mau anu, sanayende m'chilamulo chanu; sanachite kanthu ka zonse zimene munawauza achite; chifukwa chake mwafikitsa pa iwo choipa chonsechi;


Zitapita zaka zisanu ndi ziwiri mudzaleka amuke yense mbale wake amene ali Muhebri, amene anagulidwa ndi inu, amene anakutumikirani inu zaka zisanu ndi chimodzi, mudzammasule akuchokereni; koma makolo anu sanandimvere Ine, sananditchere Ine khutu.


Ndatumanso kwa inu atumiki anga onse aneneri, ndalawirira ndi kuwatuma, kuti, Bwererani kuleka yense njira yake yoipa, konzani machitidwe anu, musatsate milungu ina kuitumikira, ndipo mudzakhala m'dziko limene ndakupatsani inu ndi makolo anu; koma simunanditchere khutu lanu, simunandimvere Ine.


Chifukwa chake atero Yehova, Mulungu wa makamu, Mulungu wa Israele: Taonani, ndidzafikitsa pa Yuda ndi pa onse okhala mu Yerusalemu choipa chonsecho ndawanenera iwo; chifukwa ndanena ndi iwo, koma sanamve; ndaitana, koma iwo sanandivomere.


Koma Yeremiya anati, Sadzakuperekani. Mveranitu mau a Yehova, amene ndinena ndi inu, chomwecho kudzakomera inu, ndipo moyo wanu udzakhalabe.


Koma mau amene wanena ndi ife m'dzina la Yehova, sitidzakumvera iwe.


Koma tidzachita ndithu mau onse anatuluka m'kamwa mwathu, kufukizira mfumu yaikazi ya kumwamba, ndi kumthirira iye nsembe zothira, monga momwe tinkachitira ife, ndi atate athu, ndi mafumu athu ndi akulu athu, m'mizinda ya Yuda, ndi m'miseu ya Yerusalemu, pakuti pamenepo tinali ndi chakudya chokwanira, tinakhala bwino, sitinaona choipa.


Koma sanamvere, sanatchere khutu lao kuti atembenuke asiye choipa chao, osafukizira milungu ina.


Ndipo tsopano, chifukwa munachita ntchito zonsezi, ati Yehova, ndipo ndinanena kwa inu, ndi kuuka mamawa ndi kunena, koma simunamve; ndipo ndinakuitanani inu, koma simunayankhe;


Koma sanamvere, sanatchere khutu, koma anayenda mu upo ndi m'kuuma kwa mtima wao woipa, nabwerera chambuyo osayenda m'tsogolo.


koma sanandimvere Ine sanatchere khutu lao, koma anaumitsa khosi lao; anaipa koposa makolo ao.


Koma anapandukira Ine, osafuna kundimvera Ine, sanataye yense zonyansa pamaso pake, sanaleke mafano a Ejipito; pamenepo ndidati ndiwatsanulire ukali wanga, kuwakwaniritsira mkwiyo wanga m'dziko la Ejipito.


Musamakhala ngati makolo anu, amene aneneri akale anawafuulira, ndi kuti, Atero Yehova wa makamu Bwereranitu kuleka njira zanu zoipa, ndi machitidwe anu oipa; koma sanamve, kapena kumvera Ine ati Yehova.


Koma anakana kumvera, nakaniza phewa lao, natseka makutu ao, kuti asamve.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa