Yeremiya 1:16 - Buku Lopatulika16 Ndipo ndidzanena nao za maweruzo anga akuweruzira zoipa zao zonse; popeza anandisiya Ine, nafukizira milungu ina, nagwadira ntchito za manja ao. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201416 Ndipo ndidzanena nao za maweruzo anga akuweruzira zoipa zao zonse; popeza anandisiya Ine, nafukizira milungu ina, nagwadira ntchito za manja ao. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa16 Ndidzatulutsa mlandu wanga wotsutsa anthu anga, chifukwa cha zoipa zimene adachita pakundisiya Ine. Adafukiza lubani kwa milungu ina, namapembedza zimene adapanga ndi manja ao. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero16 Ndidzatulutsa mlandu wanga ndi iwo chifukwa cha zoyipa zimene anachita pondisiya Ine. Iwo anakafukiza lubani kwa milungu ina, ndi kupembedza zimene anapanga ndi manja awo. Onani mutuwo |
Koma tidzachita ndithu mau onse anatuluka m'kamwa mwathu, kufukizira mfumu yaikazi ya kumwamba, ndi kumthirira iye nsembe zothira, monga momwe tinkachitira ife, ndi atate athu, ndi mafumu athu ndi akulu athu, m'mizinda ya Yuda, ndi m'miseu ya Yerusalemu, pakuti pamenepo tinali ndi chakudya chokwanira, tinakhala bwino, sitinaona choipa.